Chichewa

Aniva alingalira zosumira boma

Listen to this article

Eric Aniva yemwe adaseweza chifukwa chokhala fisi ku Nsanje wati akulingalira zosumira boma pomugwiritsa jere chonsecho amangotsatira chikhalidwe.

Aniva, yemwe adatuluka kundende pa 3 April 2018 atakhala kundende zaka ziwiri atamupeza wolakwa pamlandu wotsata zikhalidwe zoipa. Iye adakhala akuchita za ufisi ndi amayi m’maboma a Nsanje ndi Chikwawa kuyambira mu 1985, ndipo adavomereza kuti adagona ndi amayi oposa 100 ndipo amalandira K5 000 kapena K10 000.

“Atangondigamula kuti ndipite kundende, loya wanga adati achita apilo koma mpaka pano palibe chidachitika. Ndikupempha akufuna kwabwino andithandize kuti chilungamo chioneke chifukwa ndinkangotsatira chikhalidwe chathu basi,” adatero iye.

Padakalipano, Aniva adachoka m’mudzi mwa Chiphwembwe kwa Senior Chief Malemia m’boma la Nsanje ndipo akukhala kwa Mbenje, T/A Ngabu m’nomalo. Iye adakhazikitsa gulu lothandiza kufalitsa mauthenga opewera matenda a Edzi.

Kaliati: Tikakumana kukhoti

“Ndikusowa chithandizo kuti ntchitoyi ndipite nayo patali komanso ndikukhala mwa umphawi,” adatero mkulu wa zaka 54.

Nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pantchito Patricia Kaliati adati boma ndi lokonzeka kukakumana ndi Aniva kukhoti.

“Amayi ali ndi ufulu wogona ndi aliyense amene iwo angakonde, koma zobisalira ku chikhalidwe n’zachikale ndipo n’zosaloledwa pomwe tili mu ulamuliro wa demokalase,” adatero Kaliati.

Kaliati adati unduna wake uli ndi maloya oimira amayi amene achitiridwa nkhanza. Amayiwo azithandizidwa mwaulele pofuna kuthana ndi nkhanza.

Koma mmodzi mwa anthu a m’deralo, Michael Dansa adati Aniva adangoperekedwa ngati nkhosa.

“Chigamulo chija chidakomera mbali imodzi. Bwanji mafumu ngakhalenso amayi ndi asungwana amene amatsata chikhalidwecho sadatengedwe? Nthawi zinanso ngati fisi angagwira ntchitoyo abale a mkazi atavomereza, onsewo adawasiya bwanji?” adadabwa Dansa.

Iye adati anthuwo amachita kukamupeza pakhomo pawo.

Koma gogo Malemia adanenetsa kuti izo adachita Aniva zidanyazitsa dera lake.

“Ndi ufulu wa aliyense kupita kukhoti kukafuna chilungamo. Komatu Aniva amatsata chikhalidwe cholakwika, n’chifukwa chake bwalo lidamupeza wolakwa litaunikira umboni komanso kupalamula kwake. Inu, munthu n’kumatchedwa bwanji kuti ndi fisi?” idadabwa mfumuyo.

Malemia adati anthu asamabisalire ku chikhalidwe akufuna kuchita zolakwika zimene zingaike ena pachiopsezo chotenga kachilombo ka HIV.”Mafumu timasunga chikhalidwe koma timalimbikitsa chikhalidwe chabwino monga mavalidwe, zakudya, zilankhulo ngakhalenso magule. Koma izi ayi,” adatero iye.

Aniva adapezeka wolakwa pa 22 November ndipo woweruza Innocent NeBi adagamula kuti akasewenze kwa zaka ziwiri, ngakhale iye adaukana mlanduwo.

Woimira boma panthawiyo Chiyembekezo Banda adati Aniva akasewenze chifukwa amatsata khalidwe limene likadaika ena pa chiopsezo chotenga matenda a Edzi.

Michael Goba Chipeta, yemwe adaimira Aniva adapempha bwalo kuti limukhululukire chifukwa chitonzo chomwe adapeza panthawiyo chidali chokwanira.

Related Articles

Back to top button
Translate »