Nkhani

Anjata wopezeka ndi mitengo ya tsanya

Listen to this article

Apolisi ku Lilongwe Lachitatu adanjata nzika ya ku China chifukwa chomuganizira kuti adapezeka ndi mitengo ya tsanya yomwe nzikayo imafuna kutumiza kwawo kuti ikasake misika.

Nzikayi adaigwira pabwalo la ndege la Kamuzu International Airport dzuwa lili paliwombo pamalo ochitira chipikisheni pabwalo la ndegelo ndipo akuti katunduyo amafuna kumukwenza ndege yopita kwawo kudzera ku Ethiopia.arrest

Apolisi a pabwalo la ndegelo adati mkuluyo, Lin Jie, adavomera mlanduwo ndipo adati mitengo yomwe amafuna kutumiza kwawoko idali yokafufuzira msika chabe kuti msikawo ukapezeka, ayambe bizinesi yotumiza mitengoyi kwawo.

“Yemwe amatanthauzira pakati pa apolisi ndi mkuluyo, Shi Qi Bine, adanena mosapsatira kuti iye amafuna kuyamba bizinesi yogulitsa mitengoyi kunja ndipo yomwe amatumizayo idali yokangoonetsa chabe,” adatero Sapulani Chitonde, mneneri wa polisi pabwalo.

Iye adati Lin Jie adauza apolisiwo kuti dziko la Malawi likufunika anthu ngati iye amasomphenya ofuna kupeza njira zina zopezera ndalama osati kudalira njira zamgonagona.

Mkuluyu adabwera m’dziko muno mwezi wa May chaka chino ndipo amakhala mumzinda wa Lilongwe.

Malingana ndi malamulo a dziko lino, ndi mlandu kupezeka ndi zam’nkhalango popanda chilolezo chilichonse ndipo apolisi ati adzathana ndi aliyense wopezeka ndi katundu wam’nkhalango mwachinyengo kapena wofuna kutulutsa katundu woletsedwa kudzera pabwalo la ndegeli.

Kumapeto a mwezi watha, apolisi adagwira nzika inanso ya ku China aipeza ikufuna kuzembetsa minyanga ya njovu yoduladula mapisi n’kuibisa m’chikwama ndi cholinga choti apite nayo kwawo.

 

Related Articles

Back to top button