Chichewa

‘Ankadzapepesa maliro a mkazi wanga’

 

Imfa ya mkazi kapena mwamuna wako si mathero amoyo. Mulungu amakoza njira ina kuti akupepese bwinobwino ndipo uyiwale zakale.

Iyi ndiyo nkhani ya momwe Excello Zidana mkonzi wa pologalamu ya Ulimi Walero adakumanirana ndi Keterina Mtambo, mphunzitsi pa Kamalambo FP School kwa Jenda ku Mzimba.

Keterina poyamba adakwatiwa ndi mbusa yemwe adamwalira zaka 7 zapitazo. Nayenso Excello adataya mkazi wake zaka zitatu zapitazo.

Excello ndi Keterina lero ndi banja
Excello ndi Keterina lero ndi banja

Awiriwatu adakumana mu November 2013, apa Excello amapita ku Karonga kukagwira ntchito. Monga mkazi wa mbusa, Keterina adali ataiwala za imfa ya mwamuna wake ndipo adayamba kutonthoza Excello paimfa ya mkazi wake.

Kupatula kutonthoza, Keterina adalimbikitsa Excello ndi mawu a Mulungu, osadziwa kuti mawa awiriwa atonthozana zenizeni pokhala mayi ndi bambo Zidana.

Kuchoka apo, awiriwa akuti adagawana manambala kuti azilimbikitsana komanso kuchezerana kufikira mu January 2015 pamene nkhani idasintha. Chikondi chidayamba kumera pamtima pa aliyense, kodi Mulungu akufuna titani?

“Mu March 2015, ndidaganiza zomuyendera, kukangozindikira kuti ali ndi chilichonse chomwe ndimafuna…..nditadzamuyenderanso mu May 2015, oh…ndiye mtima wanga kuferatu chifukwanso patsikulo adandikonzera nkhomaliro.

“Basitu Keterina adangoti zitero monga momwe mukufunira….zonse zidatheka kuti basi tizikapepesana tokha pakuti tonse tidakumana ndi mavuto,” adatero Zidana.

Pamene amakumana nkuti aliyense ali ndi ana atatu, pano poti awiriwa ndi thupi limodzi ndiye kuti banjali lili ndi ana 6 omwe ati akumvana motheratu.

Chinkhoswe chidachitika mu July ndipo ukwati wachitika pa 1 November, 2015 ku Likuni mumzinda wa Lilongwe.

Keterina amachokera m’mudzi mwa Namasasa kwa T/A Mwabulambya ku Chitipa. Excello ndi wa m’mudzi mwa Mtherereka T/A Namkumba m’boma la Mangochi.

Related Articles

Back to top button