Nkhani

Anthu 50 000 akutenga HIV chaka chilichonse

Listen to this article

Pamene nkhondo yolimbana ndi matenda a Edzi ikupitirira, zadziwika kuti chaka chilichonse anthu 50 000 akutenga kachirombo ka HIV kamene kamayambitsa matendawa.

Polankhula pamwambo woganizira anthu amene adataya miyoyo yawo kaamba ka nthendayi komanso amene ali ndi kachirombo koyambitsa nthendayi, wachiwiri kwa pulezidenti wa dziko lino Khumbo Kachali adati aliyense ayenera kutengapo gawo kuti chiwerengerochi chitsike.

“Ndi udindo wa tonse kulimbana ndi matenda a Edzi ndipo tonse tiyenera kuyezetsa,” adatero Kachali, yemwenso ndi nduna ya zaumoyo.

Mkulu wa bungwe la UNAIDS ku Malawi Patrick Brenny adati Malawi ikuchita bwino pankhondo yolimbana ndi matendawa.

“Malawi akuchita bwino makamaka makamaka pankhani ya kadyedwe, kuchepetsa kupatsirana kwa nthendayi pakati pa mayi ndi mwana komanso ma ARV,” adatero iye.

Koma Brenny adati n’kofunika kuti Amalawi agwirane manja ndipo asatope popewa matendawa.

Pamwambowo, wogwira ntchito kuwailesi Wesely Kumwenda adati atolankhani amene adapezeka ndi HIV ayenera kubwera poyera. Iye adati ngakhale adamupeza ndi HIV zaka 10 zapitazo, alibe nkhawa, ndipo wabereka ana awiri pakatipa.

Related Articles

Back to top button