Tuesday, July 5, 2022
  • About Us
  • ImagiNATION
  • Rate Card
  • Contact Us
The Nation Online
Advertisement
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation
No Result
View All Result
No Result
View All Result
Home Chichewa Nkhani

Anthu ochuluka akufuna katemera

by Martha Chirambo
21/03/2021
in Nkhani
3 min read
0
Share on FacebookShare on TwitterShare on WhatsAppShare on LinkedinLinkedinShare via Email

Pomwe zipatala zambiri zayamba kubaya katemera woteteza ku matenda a Corona mu gawo loyamba, achipatala ati anthu ankhaninkhani  omwe sali nawo mu gawo loyambali akuonetsa chidwi chofuna kubayitsa.

Msangulutso udayankhula ndi aneneri a za umoyo ku mpoto m’boma la mzimba, ku Blantyre komanso ku Lilongwe ndipo onsewa adati akulandira anthu ambiri ofuna kulandira katemera ngakhale sali nawo mu gawo loyambali lomwe ndi la ogwira ntchito za umoyo komanso zachitetezo.

Polankhulapo mneneri wa ofesi ya za umoyo ku mppoto m’boma la Mzimba Lovemore Kawayi adati katemerayu akuyenda bwino ndipo akulandira anthu ambiri omwe sali nawo m’gawo loyamba.

“Anthuwa tikumawabweza powauza kuti nthawi yawo yolandira katemera ikadzakwana tidzawalengeza,” adalongosola Kawayi.

Iye adati ofesi yake sidalandire dandaulo lililonse kuchokera kwa anthu omwe alandira katemerayu kupatula kuphwanya m’thupi ndi litsipa zomwe zimachitika ndi katemera aliyense.

Pofika Lachiwiri, anthu 477 adali atabayitsa m’boma la Mzimba.

Ndipo wofalitsa uthenga wa za umoyo ku Blantyre, Wongani Mbale, adati  ofesi yake ikulandira anthu ambiri ochita bizinesi omwe akufuna kulandira katemera.

“Koma anthuwa tikumayetsetsa kuwalongosolera kuti nthawi yawo sinakwane ndipo akumamvetsetsa,” adalongosola Mbale.

Iye adati  anthu ambiri a m’gawo loyamba amulandira bwino katemerayu chiyambireni kulandiritsa Lolemba lapitali.

Malinga ndi Mbale, ofesi yake pofika Lachitatu, idali itapereka katemera kwa anthu 1 375.

Malinga ndi mneneri wa zaumoyo m’boma la Lilongwe, Richard Mvula anthu ofuna kulandira katemera akuchulukira ndi m’magulu a anthu omwe ali ndi matenda amgonamgona komanso omwe ali ndi zaka zopitirira 60.

“Tikungowapempha kuti adikire nthawi yawo,” adalongosola Mbale.

Malinga ndi nduna ya zaumoyo, Khumbize Chiponda, anthu 9 091 ndi omwe adali atalandira kale katemerayu pofika Lachinayi.

Iye adati gawo lachiwiri la katemerayu ndi la anthu omwe ali ndi zaka zopitirira 60, omwe ali ndi matenda amgonamgona komanso a ntchito zina monga zautolankhani.

Pofika pa March 16, anthu 32 894 ndiwo adwala matenda a Corona m’dziko muno pomwe anthu 1 088 adamwalira ndi matendawa.

Mwa anthuwa, 26 890 adachira ku matendawa kuyimira 81.8 peresenti.

Previous Post

History will absolve you, Simba!

Next Post

Malawians ripped Off on passports

Related Posts

Chilima: Change the mindset toward development
Nkhani

A Chilima abwera poyera

July 1, 2022
Nkhani

Achilima awachepetsera mphamvu zaulamuliro

June 24, 2022
Katundu wa a Mtambo adali kuseri kwa ofesi za khonsolo
Nkhani

Agona ku maofesi a khonsolo ya Mzuzu

June 4, 2022
Next Post
Passport production was recently halted

Malawians ripped Off on passports

Opinions and Columns

My Turn

Child neglect and street robbery

July 4, 2022
Editor's Note

MPs’ houses to cost taxpayers K60bn

July 3, 2022
My Thought

Women underutilise digital platforms

July 3, 2022
Big Man Wamkulu

Her body count is too high, should I dump her?

July 3, 2022

Malawi-Music.com Top10

Trending Stories

  • APM, Ntaba risk Criminal charges

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Artists revel in presidential awards

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Dubai firm cries foul

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Bank questions import substitution rhetoric

    0 shares
    Share 0 Tweet 0
  • Her body count is too high, should I dump her?

    0 shares
    Share 0 Tweet 0

  • Values
  • Our Philosophy
  • Editorial policy
  • Advertising Policy
  • Code of Conduct
  • Plagiarism disclaimer
  • Disclaimer
  • Privacy Policy
  • Terms of use

© 2022 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Politics
  • Business
  • Entertainment
  • Life & Style
    • Every Woman
      • Soul
      • Family
    • Religion
    • Feature
  • Society
  • Columns
  • Sports
  • Chichewa
  • Enation

© 2020 Nation Publications Limited. All Rights Reserved.

This website uses cookies. By continuing to use this website you are giving consent to cookies being used. Visit our Privacy and Cookie Policy.