Chichewa

Apatsidwa upangiri wa chitukuko

Listen to this article

Anthu okhala kumudzi ali ndi mphamvu komanso ufulu woitanitsa chitukuko cha mtundu wina uliwonse kudera lawo kotero kuti kudzipereka pantchitoyo ndi komwe kumafunika.

Mkulu wa bungwe la National Initiative for Civic Education (Nice) m’boma la Mulanje a Twambilire Mwalubunju ndiye adanena izi Lachisanu sabata yapitayo pamene bungwe lawo lidakayendera anthu aku dera la mfumu Chonde m’bomalo.

Malingana ndi anthu omwe adasonkhana pa mkumanowo, kuphatikizapo mfumu Chonde, ntchito zachitukuko kuderalo sizimayenda bwino kwenikweni chifukwa anthu a kumudzi sadziwa ufulu komanso mphamvu zawo pa chitukuko.

Ena mwa omwe adafika kumsonkhanowo
Ena mwa omwe adafika kumsonkhanowo

“Chitukuko chimayenda pang’onopang’ono nthawi zambiri chifukwa anthu ambiri akumudzife sitidziwa udindo, ufulu komaso mphamvu zathu pa chitukuko. Timangoona ngati kubweretsa chitukuko kudera ndi udindo wa boma, mabungwe ndi ena otero. Mwachitsanzo anthu salankhulapo akamakumana ndi mavuto osiyanasiyana monga kusowa kwa zipangizo za ulimi kapena za umoyo m’zipatala,” adatero Chonde.

Mfumuyo idaonjezera kuti nthawi zambiri ntchito za chitukuko kudera lakelo siziyenda bwino chifukwa palibe mgwirizano weniweni pakati pa anthu a kumudzi, andale komanso a mabungwe ena.

“Zimakhala zomvetsa chisoni kuona kuti anthu ena amangobwera m’mudzi kudzayamba ntchito zachitukuko popanda dongosolo lenileni. Ukafunsa amakuyankha kuti adzera ku maofesi aboma. Zotsatira zake chitukuko chikamapanda kuyenda, ndi anthu akuderako omwe amavutika osati anthu

andale kapena mabungwe,” idatero nyakwawayo.

Koma mmalo mwake, bungwe la Nice lidapereka upangiri watsopano kwa anthu akwa Chonde wa momwe angathandizire kuunika komanso kutengapo gawo pantchito za chitukuko m’dera lawo.

“Kuyambira lero, munthu, bungwe kapena wa ndale asadzabwere kuno kudzakunamizani kuti ndi katswiri wa chitukuko chifukwa katswiri wamkulu ndinu. Popanda inu kutengapo gawo kapena kufunsa ndondomeka zachitukuko kudera kwanu ngati zinthu sizikuyenda, ndiye kuti mudzaononga zinthu nokha. Inuyo ndiye ani ake chitukuko amene mukuyenera kuonetstats kuti zinthu zikuyenda,” adatero Mwalubunju.

Related Articles

Back to top button
Translate »