Nkhani

Apempha alembe aphunzitsi ena

Kadaulo pa za maphunziro a Benedicto Kondowe wati boma likusempha chisa popitiriza kusula aphunzitsi pomwe aphunzitsi ena oposa 9 000 angokhala osalembedwa ntchito ngakhale kuti aphunzitsi ngochepa m’sukulu.

Iwo adanena izi popereka ndemanga pamomwe aonera bajeti ya chaka chino yomwe adati ngakhale unduna wa zamaphunziro wapatsidwa pakulamtanda, mapulogalamu ofunikira sadapatsidwe chidwi chokwanira.

Aphunzitsi ndi ochepa m’dziko lino

Iwo adati aphunzitsi omwe adamaliza maphunziro koma akungokhala akhoza kuonjezera chiwerengero cha aphunzitsi atalembedwa ntchito koma mmalo mwake boma likungolimbikira kusula aphunzitsi omwe phindu lawo silikuoneka.

“Ine ndimaona kuti ndalama zomwe zimalowa kusula aphunzitsi n’zochuluka zoti zikhoza kukwanira kulembako ntchito aphunzitsi ena n’kuonjezera chiwerengero. Kusula aphunzitsi kutha kudzapitirira patsogolo ndalama zina zikapezeka,” adatero a Kondowe.

Koma wapampando wa komiti ya za maphunziro ku Nyumba ya Malamulo a Brainax Kaisi ati ganizoli ndi losagwira chifukwa aphunzitsi osulidwa bwino akufunikabe m’dziko muno ndipo kusiya kuwasula kungabweretse vuto lina lalikulu.

“Nkhani ikhale yoti boma lipeze njira yoti aphunzitsi omwe adasulidwa kale alembedwe ntchito osati kuimitsa kusula ena chifukwa omwe alipowo atati atengedwa ndi boma komanso sukulu zoima pazokha kukhoza kubwera vuto lina la kusowa kwa aphunzitsi,” adatero a Kaisi.

Mkulu wa nthambi ya zophunzitsa aphunzitsi ku undunawo a Misheck Munthali adati nkhani yolemba ntchito aphunzitsi omwe adasulidwa kale ikukambidwa ndiye palibe chifukwa choyimitsira kusula ena.

“Padakalipano, tikukambirana zolemba aphunzitsi a IPTE 13 ndi 14 omwedi adasulidwa kale koma angokhala. Choti ndingaonjezere n’choti ganizo losiya kusula aphunzitsi ndi losagwira,” adatero a Munthali.

Iwo adati kuchoka chaka chino kudzafika chaka cha 2024, boma likufunika kusula aphunzitsi 20 000 kuti tidzafike pamlingo woyenera wa mphunzitsi ndi ana omwe amayenera kuyang’anira.

“Chaka chino chokha tisula magulu awiri, IPTE 16 ndi 17 chifukwa chaka chatha tidadumpha. Pano, mphunzitsi mmodzi amayang’anira ophunzira 67 mmalo mwa 60 ndiye ndi zovuta kwambiri. Aphunzitsi akufunika,” adatero a Munthali.

Koma Kondowe adati ngakhale mabuku a boma amasonyeza kuti ophunzira 67 amakhala ndi mphunzitsi mmodzi, m’makukamu si zili choncho chifukwa kalasi imodzi ya boma imakhala ndi ophunzira oposa 100 ndipo sukulu zina za kumudzi mumakhala ana 250.

“Boma lidalonjeza kuti lichotsa chiwerengero cha ophunzira 60 pa mphunzitsi mmodzi kufika pa 40 koma izi sizidatheke ndipo tsogolo lake silikuoneka,” adatero iwo.

Iwo adati pamwamba pa K327.3 biliyoni, unduna wa zamaphunziro ukufunika K20 biliyoni yoonjezera yothandizira kuti ntchito yolimbana ndi matenda a Covid-19 kuundunawu iziyenda komanso kontilakiti ya aphunzitsi omwe adalembedwa kwa kanthawi kochepa awonjezeledwe.

“Pali aphunzitsi apadera omwe adathandiza kuchepetsa kushota kwa aphunzitsi koma makontilakiti awo akupita kumapeto. Pakufunika ndalama zoonjezera makontilakiti amenewo,” adateroa Kondowe.

A Munthali adati anthu asadandaule za kusula kapena kulemba ntchito aphunzitsi chifukwa ndi mapulogalamu awiri osiyana omwe ali ndi bajeti zosiyana ndipo ina siyingasokoneze intake.

Related Articles

Back to top button