Nkhani

Apempha mafumu kuunika miyambo

Listen to this article

Boma komanso nthambi ya mgwirizano wamaiko wa European Union (EU) atsindika kufunika koti mafumu aunikenso miyambo ina yomwe ikadatsatidwa m’zigawo zosiyanasiyana m’dziko muno.

Mfundo iyi ndiyo idatenga gawo lalikulu la msonkhano wa masiku awiri m’sabata yangothayi wa mafumu akuluakulu ku Golden Peacock mumzinda wa Lilongwe.

Lukwa: Miyambo ina isinthe
Lukwa: Miyambo ina isinthe

Cholinga cha msonkhanowo chidali chofuna kupereka mpata kwa mafumuwa kukambirana za malamulo omwe mafumu amatsata poyendetsa zinthu m’madera mwawo koma kudaoneka kuti milandu yambiri yomwe imafuna malamulowa imakhudzana ndi miyambo.

Nduna yoona kuti pasamakhale kusiyana pakati pa abambo, amayi, anyamata ndi asungwana Jean Kalirani adanena motsindika kuti amai ndi ana ambiri amachitiridwa nkhanza zikuluzikulu kaamba kofuna kukwaniritsa miyambo ina.

“Nzoona kuti mpaka pano tizikhala tikukamba za miyambo monga kulowakufa, kuchotsa fumbi, phwando la nkhandwe ndi fisi? Zonsezi zikuchitika m’madera momwe mafumu amakhala ndipo ali ndi mphamvu zosintha zinthu,” adatero Kalirani.

Iye adati Malawi ngati dziko limodzi lomwe lidalowa nawo mumgwirizano wa maiko, ali ndi udindo oonetsetsa kuti zomwe maikowo adagwirizana zikutsatidwa ndipo chimodzi mwa mapanganowo nkuonetsetsa kuti nkhanza kwa amai ndi ana zatha.

Woimira bungwe la United Nations (UN) Ama Sande adati iye ndi nthumwi zina za kunthambi ya amayi mu mgwirizano maiko a dziko la pansiwu adagwidwa ndi chisoni atayendera madera ena nkupeza asungwana achichepere omwe adawafotokozera za momwe amakakamiziridwa kugonana ndi akuluakulu.

Iye adati adakhudzidwa kwambiri akuluakulu ena omwe adacheza nawo atawayankha poyerayera kuti mwana ndi wa zaka 8 koma akafika zaka 12 ndiye kuti wakula.

“Chomvetsa chisoni kwambiri nchakuti zambiri mwa nkhanza zomwe asungwana adafotokoza zimachitika kaamba ka miyambo yomwe imatsatidwa m’madera awo,” adatero Sande.

Senior Chief Lukwa ya ku Kasungu idati zomwe adanena akuluakuluwa nzoona ndipo adalonjeza kuti pamsonkhanowo mafumu akambirana za mfundo zokhwima zotetezera amayi ndi ana chifukwa chamiyambo.

Iye adati kuti izi zitheke nkofunika kuganizira mafumu pankhani yamayendedwe komanso ndalama zogwirira ntchito yawo mosavuta chifukwa nthawi zambiri amalephera kufikira anthu omwe akuzunzika kaamba kosowa pogwira.

Woyang’anira zakayendetsedwe ka ntchito kuunduna wa maboma ang’onoang’ono Norman Mwambakulu adalimbikitsa mafumuwo kuti ali ndi mphamvu zopanga malamulo omwe Nyumba ya Malamulo ikhoza kungovomereza.

“Zambiri zomwe aphungu a ku Nyumba ya Malamulo amakambirana nkuvomereza kuti zilowe m’bukhu la malamulo zimachokera kwa inu choncho muli ndi mpata onse okambirana zakupsa,” adatero Mwambakulu. n

Related Articles

Back to top button
Translate »