Chichewa

Apereka bajeti lolemba

Listen to this article

Nduna ya zachuma Joseph Mwanamvekha alengeza ndondomeko ya chuma yomwe boma lakonza kuti ligwiritse ntchito m’chaka cha 2019/20 Lolemba pa 9 September 2019.

Malinga ndi kalaliki wa Nyumba ya Malamulo, Leonard Mengezi, ndunayi ikadzapereka ndondomekoyo, kudzakhala misonkhano ya makomiti kukambirana za bajetiyo aphungu asadayisanthule.

Koma kadaulo pa zachuma Chiku Kalilombe wati ndondomekoyo ikuyenera kulunjika momwe muli mabala kuti ikhale ya phindu.

Mwanamvekha kupereka bajeti mwezi wa June

Iye wati boma likuyenera kuvomereza kuti zinthu zina zasokonekera m’dziko muno ndipo n’zoyenera kukonza, koma yankho lake ndi ndondomeko ya zachuma.

“Mavuto ndiye alipo monga a zaumoyo, maphunziro komanso kunjaku kukuoneka kuti chaka chino kuli njala yadzaoneni.

“Ndikhulupilira kuti bajetiyi isoka mabala amenewa apo ayi, Amalawi ali pamoto oopsa kwambiri,” watero Kalilombe.

Iye watinso kupatula pa izi, boma liunikenso bwino nkhani ya misonkho yomwe makampani amapereka kudziko ngati njira yokopera ochita malonda.

“Dziko limayenda ndi misonkho koma ngati opereka misonkhowo sakuoneka, zotsatira zake ndi mavuto. Anthu ndi makampani amathawa misonkho ikakhala yoluma kwambiri n’kupita komwe angakapeze phindu pa bizinesi yawo,” watero Kalilombe.

Kwatswiri pa zamalimidwe Tamani Nkhono Mvula wati aphungu asayiwale kukambirana nkhani ya njala pomwe zawoneka kale kuti anthu ambiri akhudzidwa ndi vutoli chaka chino.

“Tikunena pano chimanga chakwera kale mtengo moti Amalawi ambiri makamaka a kumudzi sangakwanitse kugula. Zikhala zopanda nzeru kuti aphungu akangokambirana za chuma osakhudza nkhani ya njala yomwe ikhudze anthu omwe adawavotera,” watero Mvula.

Iye wati bajeti ikangodutsa, unduna wa zamalimidwe uyambiretu kukonzekera ulimi wa 2019/20 potsatira ndondomeko zomwe zilipo kale.

Pafupifupi theka la ndalama zomwe zimapita kuunduna wa zamalimidwe, limapita ku pulogalamu ya zipangizo zotsika mtengo koma Mvula wati chimakhala chogwetsa ulesi kuti zipangizozo zimapezeka nthawi yotayika chifukwa chosakonzekera bwino.

Malingana ndi Mengezi, pamkumanowu padzakhala nthawi yapadera yokambirana mfundo zikuluzikulu ngati izi komanso kuunika malamulo ena kuti asinthidwe ngati nkoyenera.

Related Articles

Back to top button