Nkhani

Apha mkazi ndi apongozi kaamba kothetsa banja

Listen to this article

Mnyamata wina wa ku Mangochi wagwa m’manja mwa apolisi atapha mkazi ndi apongozi ake kaamba kothetsa banja.

Stephen Sani wa zaka 25 adavomera mlandu wopha mkazi wake Annie Smoke ndi apongozi ake, Enifa Smoke, ndipo pomwe timasindikiza nkhaniyi n’kuti iye akuyembekezera kukaonekera ku khoti.

Sani adati adachita zaupanduzo kaamba koti makolo a mtsikanayo adathetsa banja lake ndi cholinga choti akapitirize maphunziro.

Mayi ndi gogo wa ophendwawo, Alida Moyenda, adati awiriwo adalowa m’banja atachimwitsana. Panthawiyo n’kuti Annie ali ndi zaka 16, komanso ali folomu 1.

Gogo Moyenda adati poona kuti mtsikanayo adali wamng’ono, komanso wanzeru kwambiri pamaphunziro adaganiza zomubwezera kusukulu, koma mwamunayo adakana.

“Timafuna Annie apitirize maphunziro, koma popeza mwamunayo amakana tidangoganiza zothetsa banja kuti pasakhale kupingana kulikonse,” adatero gogoyu.

Iye adati banja la awiriwo lidatha pa August 5 2017 ndipo mtsikanayo adakayambiranso sukulu. Gogoyu adati banja la Sani ndi Annie mudalibe mavuto ena aliwonse, koma chomwe makolowo amafuna ndi choti mkaziyo aphunzire.

“Padalibe mavuto ena aliwonse, koma chomwe chimatikhudza n’choti mtsikanayo adali wang’ono woyenera kukhala pasukulu osati pabanja,” adatero Moyenda.

Mneneri wa polisi wa m’boma la Mangochi, Amina Tepani Daudi, adati pa August 13 2017 Annie ndi amayi ake adatengana ulendo wokaona mbale wawo wina m’mudzi mwa Mbapi m’boma lomwelo.

Popeza mwamunayo amakhala moyandikana ndi makolo amtsikanayo, adadziwa za ulendowo ndipo adawatsatira mpaka pa famu ya Funwe pomwe adawaimitsa ndi kuwachita chiwembu.

“Titalandira uthenga woti mu famu ya Funwe mwapezeka mitembo iwiri, tidaitengera ku chipatala chaching’ono cha Monkey Bay komwe adatiuza kuti anthuwo adamwalira kaamba ka kutaya magazi kwambiri atabaidwa ndi mipeni pakhosi,” adatero Daudi.

Iye adati apolisi adagwira Sani pomuganizira kuti ndiye adachita zaupanduzo. Atamufunsa, adavomera mlanduwo moti akuyembekezera kuyankha mlandu wakupha womwe ukutsutsana ndi ndime 209 ya malamulo a dziko lino.

Akapezeka wolakwa, Sani akagwira ndende moyo wake wonse.

Mkazi wa mtsogoleri wa dziko lino, Gertrude Mutharika, wakhala akulimbikitsa atsikana omwe adalowa m’banja akadali a ang’ono kuti abwerere kusukulu.

Malingana ndi kafukufuku wa mabungwe osiyanasiyana kuphatikizirapo la UNDP, atsikana ambiri m’dziko muno amalowa m’banja asadafike zaka 18.

Mkulu wa bungwelo, Dan Odallo, adati vutoli ndi lomwe likuchititsa kuti atsikana ambiri azisiira panjira sukulu.

“Pafupifupi theka la atsikana a m’dziko muna amalowa m’banja asadafike zaka 18,” adatero Odallo.

Pofuna kuthana ndi vutoli, Nyumba ya Malamulo idakhazikitsa malamulo woti atsikana azilowa m’banja akakwana zaka 18 kapena kupotsera apo.

Related Articles

Back to top button