Chichewa

Aphangirana ufa

 

Mwambo wa mapemphero Achisilamu otchedwa dawa udasokonekera kwa Chitulu kwa T/A Mwambo m’boma la Zomba Loweruka pa 2 April pomwe khwimbi la anthu lidakhamukira kumeneko kukalimbirana ufa womwe amati agawe mwambowo ukatha.

Kuderalo kudafika bungwe la Eid Charitable la m’dziko la Qatar lomwe limachititsa mapemphero Achisilamu ndipo pakutha pa mapemphero amayenera kugawa ufa kwa Asilamu ndi anthu ena ovutika.

Asanayambe kugawa chakudyacho amayamba ndi mapemphero a dawa ndi kupereka mwayi kwa ofuna kulowa Chisilamu kuti atha kutero povomereza kuti Muhammad ndiye mneneri wa Mulungu womaliza.

Mapemphero akupita kumapeto, Asilamuwa adapempha anthu amene ankafuna kulowa Chisilamu kuti anene pemphero loti “Ashihadu anla ilaha llah. Wa a shadu anna Muhammad u rrasulu llah” (Ndikuikira umboni kuti pali Mulungu mmodzi yekha. Ndipo ndikuikiranso umboni kuti Muhammad ndi mtumiki wake womaliza).

Khwimbi la anthu kudikira kuti alandire kangachepe
Khwimbi la anthu kudikira kuti alandire kangachepe

 

Apa mpomwe gulu la anthu ambiri, ena mwa iwo Akhrisitu, adanena nawo pempheroli ndi kuvomereza kuti alowa Chisilamu, adatero Shehe Mustapha Saidi, yemwe amayang’anira mzikiti wa Chitulu.

Mwambo wa dawa uli mkati, galimoto yomwe idanyamula ufawo idatulukira, zomwe zidayambitsa kuti khwimbi la anthu likhamukireko ndipo padali ali n’mwana agwiritse pomwe amati ayambe kugawa ufawo.

Mwina poona kuti suwakwana onse, zidavuta kuti akhale pamzere ndipo ena adayamba kukwera okha pamwamba pa loleyo kukadzithandiza okha potenga matumba a ufa. Ena amatenga awiri ena atatu amene, olemera makilogalamu 25 limodzi.

Martin Umi, wa m’mudzi mwa Chitulo, akuti iye ndi Mkhristu koma adalumbira nawo ponena pemphero la Chisilamulo kuti alandire nawo ufa.

“Kunena zoona ndidavomereza kuti ndalowa Chisilamu koma ndimangofuna kuti ndilandire nawo ufawo chifukwa cha njala pakhomo panga. Komabe mwina mtsogolomu ndilowadi Chisilamu, nanga si anthu amene akutithandiza,” adatero Umi.

Iye adati adakwanitsa kutenga matumba awiri, koma adavulala atapondedwa pamene amathawitsa ufawo.

Mfumu Chitulu idati kudera lake komanso madera ena kuli njala yadzaoneni chifukwa mvula idasiya kugwa mu January kupangitsa kuti chimanga chipserere.

“Momwe njala yavutira kuno, nkovuta kuti wina angatsale pakhomo atamva kuti kwina kukubwera chakudya. Si zodabwitsa kuona kuti anthu adaphangirana ufawo,” idatero mfumuyi, yomwe m’mudzi mwake muli anthu 1 470, omwe ndi mabanja 240.

Shehe Saidi adati chipwirikiticho chidakhumudwitsa mamembala awo amene sadalandireko ufawo.

“Zachisoni kuti mamembala athu ambiri sadalandire nawo ufawo, zomwe zachititsa kuti ena asiye kutumiza ana awo kumadrasa [sukulu ya ana ophunzira Chisilamu],” adatero Saidi, yemwe adati akuyembezabe kuona ngati omwe amati alowa Chisilamu patsiku logawa ufalo abwere kumzikiti kudzapemphera.

“Si bwino kunamizira kulowa mpingo kaamba koti ukufuna chithandizo cha kuthupi koma uzilowa mpingo kaamba kofuna kukapulumuka kumwamba,” adaonjezera Shehe Saidi, pouza Msangulutso Lachisanu lapitali.

“Lero Lachisanu olo mmodzi mwa omwe adati alowa Chisilamu patsikulo palibe amene wabwera kumapemphero. Amatero?”

Bungwe la Eid Charitable lidabweretsa ufa m’dziko muno womwe udagawidwa m’boma la Zomba, Machinga ndi Mangochi.

Mkulu wa gululi, Ali Muhammad Al-saaq, adati adauzidwa ndi bungwe la Zamzam Foundation la ku Malawi za mavuto amene Amalawi akukumana nawo kaamba ka njala.

“Titamva za mavutowa, tidabwera ndi ufa kuti ovutika athandizike. Tipemphenso anthu ena kuti athandize dziko lino. Ifeyo tikabwerera tikasakanso thandizo lina ndipo tipitiriza kuthandiza dziko lino,” adatero Al-saaq.

Iye adati ntchito yawo ndi kuthandiza ovutika komanso achipembedzo chawo cha Chisilamu powamangira mizikiti. n

Related Articles

Back to top button
WordPress › Error

There has been a critical error on this website.

Learn more about troubleshooting WordPress.