Nkhani

Aphungu akumana komaliza

Listen to this article

Nthawi yatha. Aphungu a Nyumba ya Malamulo amene adasankhidwa mu 2014 akumana komaliza kuyambira Lachiwiri likudzali Amalawi asanavote pachisankho cha patatu pa 21 May chaka chino.

Mwa zina, aphunguwo akakambirana za momwe ndondomeko ya zachuma ikuyendera kuchokera pomwe adaikhazikitsa chaka chatha komanso kumanso kukambirana mabilo ena. Izi zikutanthauza kuti nyumbayi akamaitseka, aphungu ena sadzabwereranso m’nyumbayo ngati atalephera pachisankhocho.

Aphungu m’Nyumba ya Malamulo mmbuyomu

Izi zili apo, akadaulo pa zachitetezo, ndale ndi maufulu ati msonkhano womaliza wa aphunguwo sukhala wa phindu ngati aphungu sakambirana za kubedwa ndi kuphedwa kwa anthu achialubino komwe kwayala nthenje m’dziko muno.

Akadaulowa ati izi zikhoza kutheka ngati aphunguwa atagwiritsa ntchito msonkhanowu popeza njira zokhwimitsira chitetezo cha anthu omwe ali ndi khungu la chialubino omwe chitetezo chawo chagwedezeka.

Mmodzi mwa akadaulo pa zachitetezo, Brigadier General Marcel Chirwa yemwe adakhalapo msilikali komanso Kazembe wa dziko lino adatanthauzira chitetezo cha munthu ngati kukhala mosaopa ndi kusaphwanyiridwa ufulu uliwonse.

“Chitetezo cha munthu ndi pomwe munthuyo akukhala mwaufulu wosaopsezedwa mwanjira iliyonse monga kuphedwa, njala kapena matenda. Mwachidule, chitetezo ndi pomwe munthu akukhala mosatokosedwa kunyumba, kuntchito kapena m’mudzi,” adatero Chirwa.

Iye wati aphungu akamakumana akuyenera kuunika momwe anthu akukhalira m’dziko muno makamaka omwe ali ndi khungu la chialubino n’kupeza njira zothetsera mavuto omwe anthuwa akukumana nawo makamaka pa nkhanza zobedwa ndi kuphedwa.

“N’zachidziwikire kuti anthu achialubino alibe chitetezo chifukwa akukhala mwa mantha ndi nkhanza zomwe akukumana nazo. Aphungu atakonza apa pamsonkhano wawowu, akhoza kuonetsa kukhwima nzeru kwawo,” watero Chirwa.

Katswiri pa ndale George Phiri wa ku University of Livingstonia (Unilia) wati dziko lonse lili maso pa Malawi kuti njira yothetsera nkhanza zomwe akukumananazo anthu achialubino ichokera pati moti yemwe angabweretse njirayo adzalandira ulemu waukulu.

Phiri wati aphungu a ku Nyumba ya Malamulo asenza chiyembekezo cha dziko lonse kuti mwina muzokambirana zawo zomalizazi mukhoza kutuluka njira yosowayi.

“Aphungu ali n’kuthekera kowongola zinthu pankhani ya maalubinoyi. Msonkhano uwu ndi womaliza ali pampando koma ndiokwanira kukambirana njira yotetezera maalubino moti akamakumana akuyenera kugwiritsa ntchito mpata umenewu,” watero Phiri.

Wapampando wa mgwirizano wa mabungwe olimbikitsa zaufulu Timothy Mtambo wati mabungwe ayesetsa kukankhirira kuti aphungu asalephele kukambirana zachitetezo cha maalubino mpaka njira ipezeke.

“Ngati mumatitsatira, muyikira umboni kuti takhala tikulimbana ndi boma pa zachitetezo cha maalubino koma tsopano taona mpata wina mumsonkhano wa aphungu womwe ukudzawu. Tiyesetsa kuti msonkhano umenewu usathe asadakambirane nkhaniyi,” watero Mtambo.

Nyumba ya Malamulo idasintha lamulo lokhudza kupezeka ndi ziwalo za munthu m’chaka cha 2016 pofuna kukhwimitsa chitetezo cha anthu achialubino omwe nkhani ya kuzunzika kwawo idayamba kutchuka mchaka cha 2014.

Lamuloli limati ndi mlandu kupezeka ndi ziwalo za munthu ndipo chilango chake ndi moyo wonse kundende ukugwira ntchito yakalavula gaga popanda mwayi wolipira chindapusa.

Wapampando wa komiti yoona za malamulo m’Nyumba ya Malamulo Maxwell Thyolera wati cholinga china cha lamuloli n’kuunikira kuti milandu yotere izikambidwa m’khothi lalikulu osati m’makhothi ang’onoang’ono a majisitileti.

“Nkhawa yathu ndi yoti apolisi ndi makhothi sakugwiritsa ntchito lamuloli mokwanira chifukwa tinkayembekezera kuti nkhani zotere zichepa kapena kutheratu ndi lamuloli,” watero Thyolera.

Pano, makomiti atatu; ya zamalamulo, chitetezo ndi makhalidwe a anthu m’madera akhazikitsa komiti imodzi yoti ifufuze chomwe chikuchitika pa nkhani zozembetsa ndikupha maalubino ndipo ati zotsatira zakafukufukuyu zidzaperekedwa m’Nyumba ya Malamulo.

Kuchoka m’chaka cha 2014, milandu yokhudza kuzembetsa ndi kupha maalubino chidafika pa 152 yomwe ikuphatikiza 25 ya maalubino ophedwa ndi ena 14 omwe akusowa. n

Related Articles

Back to top button