Nkhani

Aphungu asaiwale kukambirana za njala

Listen to this article

Pomwe kwangotsala masiku 9 kuti aphungu a ku Nyumba ya Malamulo akakumane kukambirana za momwe ndondomeko ya chuma yayendera pa miyezi 6 yapitayi, mabungwe ndi mafumu ena ati nkhani ya njala isakalephere kukambidwa.

Mabungwe ndi mafumuwa ati nkhani ya njala ili mkamwamkamwa paliponse kotero kuti ikufunika kupatsidwa mpata aphunguwa akamakumana kuti papezeke njira zothandizira anthu, makamaka a m’midzi.

Chifukwa cha njala ena akuupeza pa nyanya kapena nyika
Chifukwa cha njala ena akuupeza pa nyanya kapena nyika

Mfumu yaikulu Mkukula ya ku Dowa yati kupanda kukambirana za njala ndiye kuti palibe chimene msonkhano wa aphunguwo ungaphule.

“Panopa ngakhale mwana wamng’ono akudziwa zoti njala yayamba chifukwa amazionera m’nyumba mwawo kuti zinthu sizikuyenda momwe zimakhalira nthawi zonse,” idatero mfumuyo.

Iyo idati m’misika yambiri ya Admarc chimanga chikuvuta kupeza moti anthu akuchita kugonera komweko kapena kulawirira kuti mwina apeze mwayi wogula chakudya ndipo izi zaimitsa ntchito zambiri m’midzimo.

“Mmalo molawirira kumunda kapena kudimba, anthu akulawirira ku Admarc kukadikirira chimanga. Choncho kumundako kukapanda kusamalika, chaka chamawa kudzakhala zotani? Iyi ndi nkhani yofunikira kwambiri ndipo isakalephere,” adatero Mkukula.

Iye adati kupatula kukambirana zoti chakudya chizipezeka m’misika ya Admarc, aphunguwa akakambiranenso za njira zoti anthu akapanda kukololanso bwino azidzalima chakudya china monga kudzera mu ulimi wamthirira.

Pophera mphongo, mfumu yaikulu Tsabango ya ku Lilongwe idati nkhani ya chakudya ikufunika kuikapo mtima komanso njira zoti anthu azipezera chakudya china podzera m’njira ya ulimi wamthirira.

“Ife mafumu ndiye timakhala ndi anthu m’midzimu ndiye chilichonse chikachitika chimayambirira kupeza ife. Ngakhale nkhani ya chakudya imene, ngati chimanga chikusowa m’misika, anthu amayang’ana ife,” adatero Tsabango.

Iye adati pokambirana za mmene ndondomeko ya chuma cha 2015/2016 yayendera m’miyezi 6 yapitayi, mpofunika ndithu kupeza mpata wokambiranako za chakudya ndi njira zolimira m’nyengo ya chilimwe  kuti zinthu zisadzachite kufika posauzana.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe a zaulimi la Civil Society Agriculture Network, Tamani Nkhono-Mvula, adati zomwe mafumuwa anena nzoona kutengera momwe zinthu zilili.

Iye adatchulapo kukwera mtengo kwa chimanga chomwe chili ndi mavenda, kusowa kwa chimanga m’misika ya Admarc ndi kabweredwe ka mvula ka chaka chino, zomwe adati sizikupereka chiyembekezo chokwanira kwa anthu.

Nkhono-Mvula adati pakufunika mfundo zomveka bwino komanso ndondomeko yooneka bwinobwino ya kagawidwe ka chimanga m’madera osiyanasiyana kuti m’madera onse anthu azitha kupeza chakudya uku akugwira ntchito m’minda yawo kuti chaka chamawa asadzavutike.

“Pokambiranapo, aphungu akaonetsetse kuti akhazikitsa mfundo zoteteza kuti ogulitsa chimanga m’misikayi akutsata malamulo osati kuchita chinyengo ndi mavenda omwe amafuna kuti azigula kumisikayi motsika mtengo iwo n’kumakagulitsa pamtengo wokwera.

“Anthu, makamaka akumidzi, akufunika chitetezo chachikulu pankhaniyi chifukwa ambiri timamva akudandaula kuti akapita m’misika amapeza chimanga mulibe koma mavenda akupezeka nacho. Iwo msika wake amaupeza kuti?” adadabwa Nkhono-Mvula.

Pankhani ya ulimi wa mthirira, mkuluyu adati maganizo a mafumu ndi olondola potengera momwe mvula ikugwera chaka chino. Iye adati sizikudziwika kuti makololedwe adzakhala otani.

“Nkhani ya mthirira ndiye siyochita kufuna riferendamu, aliyense akudziwa kuti njira yokhayo yolimbana ndi kabweredwe ka mvula ka chaka chino ndi mthirira basi, ndiye aphungu sangakambe za njala osakambirana za mthirira,” adatero Nkhono-Mvula.

Mkulu wa mbali ya boma m’Nyumba ya Malamulo Francis Kasaila adati ngakhale mndandanda wa zokambirana za kunyumbayi sudatuluke, nzachidziwikire kuti aphungu akakambirana nkhani ya njalayi.

Iye adati pali nkhani zingapo zomwe zidatsalira pankhumano yomwe amakambirana za bajeti zomwe akukhulupilira kuti zibwereranso m’nyumbayi ndipo nkhani ya njala ndi imodzi mwa nkhani zomwe aphungu sangalekerere kukambirana.

“Ndondomeko ituluka Lachitatu komiti yomwe imakonza ndondomekoyi ikamaliza kukumana koma nzachidziwikire kuti nkhani yokhudza njala ikhalapo chifukwa ndi nkhani yofunika kwambiri,” adatero Kasaila.n

Related Articles

Back to top button
Translate »