Nkhani

Aphunzitsi adzawalabadire ndani?

Listen to this article

Ambiri timadzudzula kujombajomba komanso kusalimbikira ntchito kwa aphunzitsi m’sukulu za boma.

Mchitidwewu ngopititsa pansi maphunziro chifukwa ophunzira amachoka kusukulu asanasulidwe moyenerera.

Koma ambirife tikadakhala aphunzitsi bwenzi tikuchita zofanana kapena zoonjezanso kuponsa mmene ena achitira lero lino, maka  tikaona mmene boma limachitira ndi aphunzitsi  pa nkhani ya malipiro.

Choyamba, aphunzitsi ambiri amalandira ndalama yochepa kwambiri yomwe njovuta kufikira zofuna za munthu pamoyo wake, choncho n’zomveka ndithu kuti mphunzitsi wopereweredwayu azinka nasaka njira zina zopezera ndalama poonjezera pa malipiro ake.

N’chifukwa chake nthawi yoyenera kuti aphuzitse, ena amakhala akuthamangitsa bizinezi.

Chachiwiri, pazifukwa zosadziwika bwino aphunzitsi kawirikawiri amachedwa kulandira malipiro awo.

Pofika Lachitatu lapitali, pa 3 Julaye, aphunzitsi ena adali asadalandire salale yawo yochepa ndikaleyo.

Aka si koyamba kuti malipiro a phunzitsi achedwe. Nthawi zina masabata amadutsa malipiro a aphuzitsi asakuoneka.

Aphunzitsi afika pozolowera kuchedwaku kotero kuti akalandira munthawi yake ndalama, amadabwa.

Kodi timati aphunzitsiwa azikhala bwanji?

N’kale lija aphunzitsi adayamba kudandaula za kuchedwa kwa malipiro. N’chifukwa chiyani boma likulephera kupeza njira yoti mwezi ukamatha malipiro azikhala atakonzedwa?

Chikondi cha nkhwangwa—chomayembekeza ntchito yapamwamba kuchokera kwa aphunzitsi pamene mwezi ukatha sakulabadiridwa—n’chosathandiza.

Ndi chifukwa chake  aphunzitsi adatulukira njira yogwira ntchito molingana ndi momwe owalemba ntchito akuwasamalira.

Opwetekeka si aphunzitsi kapena owakonzera malipiro, koma ana omwe sakusulidwa moyenera. Mapeto ake dziko lathu likhalabe lotsalira chifukea nzika zomwe zikudutsa msukulu za bomazi zikhala zosaphunzira moyenera.

Mmalo moloza aphunzitsi, tiloze pomwe pakuyambira vuto—ndondomeko zogwirira ntchito za aphunzitsi n’zosakoma konse, ndipo mpovuta kuti aphunzitsi asinthe ngati izi sizikonzedwa.

Related Articles

Back to top button