Nkhani

APM alola ansah achoke

Listen to this article

Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika dzulo wavomereza kuti wapampando wa bungwe la zisankho la Electoral Commission (MEC) Jane Ansah atule pansi udindo wake.

Ansah Lachinayi adalengeza kuti adalembera Mutharika kuti akufuna kutula pansi udindowo potsata malamulo, osati kuopa zionetsero. Koma iye adaonjeza kuti Mutharikayo adali asanayankhe.

Ansah: Sindikuchoka poopa zionetsero

Koma dzulo, mneneri wa Mutharika Mgeme Kalilani adati adalola Ansah kuti atule pansi udindo wake.

“Mutharika walola kuti Ansah atule pansi udindo. Iye wayamikira Ansah pokhala mmodzi mwa Amalawi okonda kwambiri dziko lawo. Ndikuwafunira zabwino zonse konse angapite,” adatero Kalilani.

Malinga ndi malamulo a dziko lino majaji 6 mu nthambi yolemba ogwira ntchito za malamulo ya Judicial Service Commission ndiwo amasankha munthu amene akhale wapampando wa MEC ndipo mtsogoleri wa dziko lino ndiye amavomereza dzinalo. Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adavomereza dzina la Ansah pa 14 October mu 2016 ndipo kontilakiti yake imayenera kudzatha mwezi wa October chaka chino.

Mkulu wa bungwe lomenyera ufulu wa  anthu la Human Rights Defenders Coalition (HRDC) Gift Trapence adati ngakhale Ansah wachoka, zionetsero zimene anakonza kuti makomishona a MEC nawo achoke zipilirabe.

“Tikufuna makomishona onse achoke. Tikufunanso kuti tsiku la chisankho liikidwe posachedwa. Komanso boma lipeze ndalama zimene zikusoweka kuti chisankho chichitike. Ngati Reserve Bank of Malawi idapereka K6 biliyoni kuthumba lothana ndi matenda a Covid-19, zachisankho zingavute pati?” adatero Trapence.

M’sabatayi, mtsogoleri wa chipani cha UTM Party Saulos Chilima adakamang’ala kubwalo la milandu kuti Ansah achotsedwe limodzi ndi makomishona ake. Mmbuyomu, komiti ya Nyumba ya Malamulo yoona zolemba anthu m’maudindo ena a boma adalembera Mutharika kuti achotse makomishonawo koma Mutharika adakana kutero.

Padakalipano, oimira Chilima adapempha mkulu wa majaji Andrew Nyirenda kuti alole mlanduwo umvedwe m’bwalo lounikira malamulo aakulu a dziko lino la Constitutional Court.

Polankhula ndi mtolankhani wathu dzulo, woimira Chilima, Chikosa Silungwe adati kaya Ansah atula pansi udindo kaya satula, mlandu wawo ukupitirira.

“Mumvetsetse. Ifetu tikufuna bwalo lilingalire zochotsa makomishona osati Ansah yekha. Mlandu ukadalipo,” adatero Silungwe.

Mneneri wa UTM Party Joseph Chidanti Malunga adati adagwirizana ndi ganizo la Ansah. “Koma wachita izi mochedwa zinthu zitathina kale,” adatero Malunga.

Related Articles

Back to top button
Translate »