Chichewa

Apolisi adabwitsa chipani cha UTM

Listen to this article

n’chodabwa ndi momwe apolisi, komanso a bungwe la Malawi Electoral Commission (MEC) akuyendetsera madandaulo awo.

Mlembi wa chipanicho, Patricia Kaliati, adati adakatula dandaulo la kumenedwa kwa mneneri wawo, Joseph Chidanti Malunga, ku polisi ndi ku MEC koma mpaka pano palibe chomwe chachitikapo.

MEC yati ikuunikabe nkhani ya Malunga pamene apolisi akuti adauzidwa kuti nkhaniyo ipita ku komiti younika mavuto omwe zipani zandale zikukumana ya Multiparty Liaison Committee (MLC).

Kaliati kufotokoza zaupandu akukumana nazo

Kupatula nkhani ya Malunga, Kaliati adati UTM idadandaulanso ku MEC ndi ku polisi kuti membala wake mmodzi wa kwa Nkando ku Mulanje wamenyedwa, koma mpaka pano nkhaniyo mutu wake sukuoneka.

Iye adati apolisi amafulumira kuchitapo kanthu pa dandaulo la chipani cholamula cha Democratic Progressive Party (DPP).

Kaliati adapereka chitsanzo cha dandaulo la DPP loti anthu ena adagenda mdipiti wa galimoto za mtsogoleri wake, Peter Mutharika, ku Kasiya ku Lilongwe komwe amakatsegulira msewu.

Iye adati apolisi sadachedwe kumanga anthu atatu, koma pa nkhani za UTM sachitapo kanthu.

“Takhala tikupereka madandaulo athu ku polisi ndi ku MEC, koma palibe chomwe amachita. Koma anzathu a DPP akadandaula, amachitapo kanthu msanga,” adatero Kaliati.

Mneneri wa polisi, James Kadadzera, adati adauzidwa kuti nkhani ya Malunga ipita ku komiyi yomva madandaulo a zipani ya m’boma la Nsanje, koma adati sadalandire dandaulo la UTM la kwa Nkando.

“Apolisi akugwira ntchito yawo mokhulupirika. Mwachitsanzo, anyamata atatu omwe adavula mayi wa UTM ku Mangochi adamangidwa moti tikulankhula pano ali mchitokosi.

“Mlandu wa a Malunga udatipeza, koma adatiuza kuti aperekedwa ku komiti yomva madandaulo a zipani ya m’boma la Nsanje,” adatero Kadadzera.

Mneneri wa MEC Sangwani Mwafulirwa adati madandaulo onse awiri wokhudza kumenyedwa kwa Malunga ndi membala wa UTM wa kwa Nkando adalandira.

“Dandaulo la Malunga likuunikidwa, koma linalo likuyenera kupita ku komiti yomva madandaulo a zipani ya m’boma la Mulanje,” adatero Mwafulirwa.

Kadadzera adati apolisi akulandira madandaulo ochepa kaamba koti anthu adamvetsetsa mauthenga opewa ziwawa omwe mabungwe akufalitsa.

Iye adayamikira atsogoleri azipani posungitsa mwambo pakati pa achinyamata awo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »