Nkhani

‘Apolisi adalakwa pomanga aphungu’

Listen to this article

Katswiri wina wa za malamulo ndi anthu ena othirapo ndemanga agwirizana ndi bungwe la Malawi Law Society (MLS) ponena kuti kumanga phungu wa Nyumba ya Malamulo pomwe mkhumano wa Nyumbayo uli mkati ndi kulakwira malamulo a dziko lino.

Mphunzitsi wa zamalamulo kusukulu yaukachenjede ya Chancellor College, Edge Kanyongolo, wanenanso kuti kumanga anthu pogwiritsa ntchito mauthenga a pafoni n’kuwaphwanyira ufulu wawo wokhala ndi chinsinsi.mcp

Kanyongolo adanena izi m’sambatayi apolisi atagwira aphungu awiri ena a Nyumba ya Malamulo a chipani cha MCP, Peter Chakhwantha ndi Jessie Kabwila, ndi mkulu wina wa chipanichi, Ulemu Msungama powaganizira kuti amakambirana zogwetsa boma la Peter Mutharika pamauthenga a palamya otchedwa WhatsApp.

Izi zitangochitika, bungwe la maloya la Malawi Law Society (MLS) lidati apolisi adaphwanya lamulo pomanga aphunguwo masiku a zokambirana zawo asanathe.

“Gawo 21 la malamulo oyendetsera dziko lino limati aliyense ali ndi ufulu wokhala ndi chinsinsi. Lamuloli limaletsa kusechedwa opanda chikalata cha boma, kulandidwa katundu ngakhalenso kuwerengeredwa kalata komanso nkhani zonse zokhudza mafoni,” adatero Kanyongolo.

Iye adati umboni wotengedwa popanda chilolezo wotere suloledwa kukhoti ndipo ngati wina angapereke umboni wotere, akhoza kusumiridwa.

“Koma zikhoza kuvuta ngati mmodzi mwa amene amakambirana nawo izi ndiye adakapereka mauthengawo kupolisi,” adatero Kanyongolo.

Mpungwepungwe udayamba Lamulungu pomwe apolisi adamanga Msungama pomuganizira kuti akukhudzidwa ndi nkhaniyo pomwe Chakhwantha ndi Kabwila samadziwika komwe adali.

Koma Lolemba pamene msonkhano wa aphunguwo udayamba, apolisi adatchinga zipata zotulukira ku Nyumbayo koma sadathe kugwira aphungu awiriwo. Kabwila adamugwira akuti azithawira kumaofesi a kazembe wa dziko la Germany pomwe Chakhwantha adakadzipereka yekha kupolisi Lachiwiri.

Kanyongolo adati malamulo a dziko lino salola kumanga phungu pomwe mkhumano wa Nyumba ya Malamulo uli mkati.

“Ndime 60(1) ya malamulo imanena kuti phungu ali ndi chitetezo choti sangamangidwe panthawi yomwe akupita, kuchokera kapena pomwe ali ku Nyumba ya Malamulo,” adatero Kanyongolo.

Naye mphunzitsi wotchuka wa za malamulo ku Cape Town m’dziko la South Africa, Danwood Chirwa, adapherapo mphongo ponena kuti aphungu akangoyamba kukumana amakhala otetezedwa pankhani yomangidwa ngakhale kuti sali m’Nyumbamo.

“Malamulo amati aphungu sayenera kumangidwa zokambirana zikatsegulidwa chifukwa amakhala otetezedwa. Zokambirana zingatenge nthawi yaitali bwanji chitetezochi chimakhalapo koma akhoza kudzamangidwa zokambirana zikatsekedwa,” adatero Chirwa.

Mpungwepungwe wa Lachiwiriwo udachititsa sipikala wa Nyumba ya Malamulo Richard Msowoya kuimitsa msonkhano wa aphungu atamasulira kumangidwa kwa aphunguwo ngati kuchepetsa mphamvu za Nyumbayi.

“Zokambirana ziyamba zaima mpaka boma lititsimikizire za chitetezo chathu ngati aphungu a Nyumba ya Malamulo,” adatero Msowoya.

Koma mkulu wa apolisi Lexton Kachama adati apolisi sadalakwe pomanga atatuwo ndipo adati akadafufuza nkhaniyi.

“Sitidachite kutumidwa ndi andale. Anthuwo sitidawazenge mlandu wofuna kuukira boma chifukwa tidangofuna kumva mbali yawo. Ntchito yathu ngati apolisi nkusungitsa bata ndipo izi timachita mwa ukadaulo wathu,” adatero Kachama ngakhale sadafune kunena momwe adapezera mauthenga a foni za eni ake.

Mpungwepungwewu udayamba sabata yatha kumkhumano wa komiti yoona za mmene zinthu zikuyendera m’dziko ya Public Affairs Committee (PAC) mumzinda wa Blantyre komwe nthumwi za boma ndi zotsutsa boma zidasemphana Chichewa pankhani yoti Mutharika ayenera kutula pansi udindo wake ngati mtsogoleri wa dziko lino ati kaamba kolephera kupeza mayankho a mavuto a zachuma ndi kusowa kwa chimanga m’misika ya Admarc.

Kusemphanako kudabuka nthumwi zotsutsa boma zitatemetsa nkhwangwa pamwala kuti Mutharika atule pansi udindo kaamba kolephera kuyendetsa bwino zinthu.

Nkhani yomwe idavuta kwambiri ndi ya kayendetsedwe ka chuma ndi njala yomwe yasanduka mutu wa nkhani pafupifupi paliponse m’dziko muno maka pakusowa kwa chimanga m’misika ya Admarc.

Zipanizi zidapereka malire a masiku 30 kuti boma litumize chimanga m’misika ya Admarc kapena litule pansi udindo kuti ena omwe angakhale ndi njira zothetsera vutoli atenge phamvu zoyendetsa boma.

Pamkhumanowu, aphungu akuyembekezeka kukambirana za momwe chuma chikuyendera, nkhani ya njala, nkhani yokhudza ufulu wolemba ndi kufalitsa nkhani ndi mitu ina yomwe idatsalira pazokambirana za ndondomeko ya chuma cha 2015/16.

Nkhani yokhudza ufulu wa atolankhani yakhala ikuvuta ndipo ndi imodzi mwa nkhani zikuluzikulu zomwe zidabwerera pamkhumano wa ndondomeko ya chuma womwe wapitawo ndipo bungwe la atolankhani ndi maiko ena kudzera mwa akazembe awo adadzudzula kuponderedzedwa kwa nkhaniyi.

Related Articles

Back to top button
Translate »