Chichewa

Apolisi akuthetsa milandu ku Nthalire

Listen to this article

Apolisi ena ku Nthalire m’boma  la Chitipa akuweruza ndi kuthetsa milandu osaipititsa kubwalo la milandu.

Izi zidadziwika sabata yapitayi pomwe bungwe la National Initiative for civic Education (Nice) lidachititsa msokhano m’deralo.

Aka si koyamba kuti nkhani zotere ziphulike papolisipo. Mmodzi mwa akuluakulu a bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) m’bomalo, John Moyo, atalandira malipotiwo adaitanitsa mkulu wapolisiyo mwezi wa June chaka chatha.

“Tidawaitanitsa kumsonkhano umene onse okhudzidwa akadakhalako koma poyamba adati ndiwotangwanika. Tidakonza tsiku lina ndipo tidachita kukawatenga. Adavomera kuti zimalakwika ndipo adati izi zitha,” adatero Moyo.

Koma mkulu wa polisi ya Nthalire Ben Mwaliwa adati pamsonkhano watsopanowu iyeyo padalibepo.

“Ine ndikudziwa za msonkhano wa chaka chatha omwe lidakonza ndi bungwe la CCJP. Pamsonkhanowu tidalonjeza kuthetsa mchitidwewu. Mbuyomu madandaulo amenewo adalipo koma zoti pano kukumalandiridwa ndalama ndinamapo,” adatero Mwaliwa.

Atafunsidwa ngati akumatumiza milandu ku bwalo la milandu, iye

adavomera kuti polisi ya Nthalire ikumatumiza milandu kubwalo la milanduyi.

Malinga ndi ofisala wa bungweli m’boma la Chitipa, Amos Ngoma, akomiti za chitukuko komanso anthu okhudzidwa adatambasula pamsonkhano wapadera sabata yatha kuti milandu ikumathera kupolisi komwe apolisiwa akumapatsidwa ndalama potengera ndi kukula kwa mlandu.

“Apa tidapempha oweruza milandu m’derali kuti azipita kupolisi tsiku ndi tsiku kukatenga malipoti a anthu otsekeredwa m’chitokosicho kuti aziunika omwe angapatsidwe belo pasanathe maola 48,” adatero Ngoma.

Kutulutsidwa kwa anthu asanatengeredwe kukhoti kwachititsa kuti bwalo la majisitileti ku Nthalire lisamalandire milandu zomwe zikupereka mafunso kwa ena mwa anthu ogwira ntchito pabwalopo chifukwa Nthalire ndi tauni yaikulundithu, imenenso  ili m’malire a dziko lino ndi la Zambia ndipo kupalamula nkwakukulu.

Malinga ndi ena mwa ogwira ntchito pabwalopo omwe sadafune kutchulidwa maina poopa kuchitidwa chipongwe, bwaloli limayembekezera kumazenga milandu itatu kapena inayi pa tsiku.

Koma padakalipano palibe ngakhale mlandu ndi umodzi omwe ukutumizidwa kubwaloli.

“Tikakafufuza kupolisi timapeza kuti anthu ali m’chitokosi ndithu; koma milanduyi ikumathera konko,” adatero anthuwo.

Pomwe CCJP adachititsa msonkhano mu June, mfumu  Chipuwe idati mwana wake wamwamuna adauzidwa kuti apereke K60 000 kuti akatenge njinga yake yomwe idali m’manja mwa apolisi kaamba koti adachita nayo ngozi.

Ndipo nawo a bwalo la milandu pa nthawiyo adanenetsa kuti iwo adadziwa kuti china chake si chili bwino kupolisi chifukwa samalandira milandu ngati momwe zilili pano.

Mneneri wa apolisi m’chigawo cha kumpoto, Peter Kalaya, adati ngakhale ofesi ya polisi ya Chitipa ikumamvera za nkhaniyi m’misonkhano ndipo palibe wapitako kukawadandaulira za nkhaniyi.

“Pena pake tikudziwa kuti anthuwa amaopa chifukwa nkhani za katangale zimakhudza anthu awiri. Nawonso amaopa kuti ziwakhudza,” adatero Kalaya.

Iye adaonjezera kuti wapolisi akapezeka akuchita katangale amatengeredwa kubwalo la milandu komwe amakayankha mlandu wokhudza katangale. n

Related Articles

Back to top button
Translate »