Nkhani

Apolisi amanga mayi wa mwana womwa kachasu

Listen to this article

Apolisi ku Chirimba mu mzinda wa Blantyre akwizinga mayi wa mwana ndi anzake awiri powaganizira kuti amalekerera ndi kuyamikira mwana wa zaka zinayi akugwetsa matoti a kachasu.

Amayiwa adawamanga potsatira kanema yemwe amazungulira pa masamba a mchezo a Facebook ndi WhatsApp yoonetsa mwanayu akupapira kachasuyo.

An illustration of an arrest

M’malo momuletsa, amayiwa akuwaganizira kuti amamuchemerera mwanayo kwinaku akumufunsa mafunso n’kumamujambula kanemayo.

Kanemayu akuonetsa mwana akugwetsa matoti a kachasu ngati akumwa madzi kwinaku akufotokoza kuti adamuphunzitsa kupapira kachasu ndi azakhali ake aku Ndirande.

Mwanayu adagwetsa yekha botolo la kachasu la mamililita 250.

Mneneri wa polisi wa ku Blantyre, Augustus Nkhwazi, wauza Msangulutso kuti amayiwa adakaonekera ku khoti Lachitatu pa October 2 pa mlandu wochita chikhalidwe choononga ( harmful cultural practices) womwe umapezeka m’gawo 80  la malamulo oteteza ana a m’dziko muno.

Nkhwazi adati khoti latulutsa amayiwa pa belo atapereka chikole cha K40 000 aliyense.

“Koma pakadali pano  mwanayu ali m’manja mwa agogo ake mpaka mlanduwu udzathe. Akhoti adauzanso a nthambi yoona zakasamalidwe ka ana m’dziko muno kuti apeze malo wokasungirako mwanayu pa nthawi ya mlanduwu,” adalongosola Nkhwazi.

 Malipoti a ku bwalo la milandu akusonyeza kuti bambo wa mwanayu adakwiya ndi kanemayo mpaka adakasumira ku khoti amayiwo.

 Amayiwa aukana mlanduwo ndipo khoti layamba kaye laimitsa mlanduwu mpaka pa October 22 2019.

Bungwe lomenyera ufulu wa ana la Centre for Human Rights Education Advice and Assistance (Chreaa) lati ndi lokhumudwa ndi nkhaniyi.

Chaguluka Mhango, m’modzi mwa ogwira ntchito ku Chreaa, adati: “Amayiwa amadziwa kuti mwanayu akulakwitsa ndipo amayenera kumuletsa.

“Koma m’malo motero amajambula kanemayo ndi mwansangala. Apatu zikuonetseratu kuti malo womwe mwanayu akukulira siwoyenera mwana kukhalapo.”

Iye adati pakadali pano mwanayu akufunika thandizo chifukwa kachasu ndi wa mphamvu wosayenera ana kumwa. n

Related Articles

Back to top button
Translate »