Chichewa

Apolisi anjata ‘wolemba ntchito’ apolisi

Listen to this article

 

Pamene Patrick Mayeso Nkhoma wa zaka 28 ndi anzake ena 35 amanyadira kuti ayamba kuzinyambita ndalama za boma akalembedwa ntchito yaupolisi, iwo sadadziwe kuti owalemba ntchitowo, adangofuna kuwatafunira ma K9 500 awo powanamiza kuti.

Malinga ndi mneneri wa polisi ku Machinga Davie Sulumba, apolisi a m’bomali agwira Ellard Sanudi, wa zaka 32, pomuganizira kuti iye ndi mnzake wina amene pakadalipano sakudziwika komwe ali, adanamiza anthu kuti awalemba ntchito yaupolisi, zomwe zikutsutsana ndi ndi gawo 361 la milandu ndi zilango zake (Penal Code) la malamulo oyendetsera dziko lino.

ARREST

Sulumba adati Sanudi ndi mnzakeyo akuwaganizira kuti adauza anthuwo kuti apereke maina awo, masatifiketi ndi nambala za foni komanso alipire K9 500 aliyense ngati atsimikizadi kuti akufuna kulembedwa ntchito kupolisi.

“Anthuwa adalipiradi ndalamazi, ena pamanja pamene ena adalipira kudzera pa TNM Mpamba komanso Airtel Money, ndipo adawatsimikizira kuti pa 30 May chaka chino akakumane pabwalo la T/A Nsanama ku Machingako kuti akanyamuke pagalimoto ya polisi kupita kusukulu yophunzira ntchito zaupolisi,” adatero Sulumba.

Tsikuli litafika anthu ofuna ntchitowa adafika pabwalo la mfumulo mwamachawi atanyamula zikwama zawo, koma kudangoti zii ngati kumanda, Sanudi ndi mnzake osatulukira pamalopo. Izi zidachititsa anthuwa kukamang’ala kupolisi.

Pakadalipano apolisi anjata Sanudi amene akuti adali ngati kalaliki wa oganiziridwawa, pamene mnzake, amene akuti adavala yunifomu ya polisi, akusakidwabe.

“Tikupempha anthu kuti asamanamizidwe munjira ina iliyonse kuti alembedwa ntchito kupolisi panopa chifukwa pakadalipano anthu adapita kale kusukulu kukayamba maphunziro a upolisi,” adatero Sulumba. n

Related Articles

Back to top button
Translate »