Nkhani

Apolisi, mabungwe akufuna kuteteza ufulu wa ana

Apolisi ati agwirana manja ndi mabungwe osiyanasiyana pa ntchito yoteteza ufulu wa ana m’dziko muno.

Mkulu wa polisi ya Chirimba, Aubrey Chimenya ndiye adalankhula izi pamsonkhano womwe bungwe la Chisomo Children’s Club idachititsa pa sukulu ya Chirimba mu mzinda wa Blantyre.

“Mwana ali ndi ufulu wophunzira, koma n’zokhumudwitsa kuti m’malo motumiza ana kusukulu makolo akumatumiza ana awo kukagulitsa zibwente, zitumbuwa, zindasi, madonasi ndi zinthu zina,” adatero Chimenya.

Iye adati agwira ntchito ndi mabungwe osiyanasiyana kuphatikizirapo la Chisomo kuti athane ndi mchitidwewu.

“Tiziyenda m’misika ndipo tikapeza ana akugulitsa katundu m’misika tiziwaitana kuti atiuze zolinga zawo,” adatero Chimenya.

Mkulu wa bungwe la Chisomo m’chigawo cha kummwera, Auspicious Ndamuwa, adati cholinga cha bungwe lake ndi kuonetsetsa kuti ufulu wa ana ukutetezedwa.

Iye adati mwana ali ndi ufulu wopatsidwa dzina, mankhwala akadwala, kutetezedwa, kusingiridwa chinsinsi, wosonkhana ndi a mnzake, wolankhula zakukhosi ndi maphunziro.

“Ntchito yopeza ndalama zogwiritsira pakhomo si ya ana, koma makolo. Choncho makolo asaphwanye ufulu wa maphunziro wa ana powatumiza kukagulitsa malonda anzawo ali m’kalasi,” adatero Ndamuwa.

Mphunzitsi wamkulu wa pa sukulupo, ndi yemwe adaimirira nyakwawa ya mderalo adavomereza kuti ana ambiri amapezeka pa msika wa Chirimba nthawi ya maphunziro.

Related Articles

Back to top button