Nkhani

Apolisi mbweee! ku PAC

Listen to this article

Kwa munthu wongofika kumene mumzinda wa Blantyre, ngakhale nzika za mzindawu, sabata imene yangothayi kudali chitetezo chokhwima zedi pomwe apolisi adali ponseponse. Kuyambira m’mawa, apolisi adali ndi ma ‘rodibuloku’ adzidzidzi m’madera ena.

Mmodzi mwa anthu okhala ku Machinjiri, Leston Kampira, Lachitatu adati adadabwa ndi mndandanda wa galimoto umene udalipo pa Wenela.

“Tidayenda pang’onopang;ono mpaka kukafika pa Wenela kuchoka pa HHI. Tidapeza kuti apolisi amaimitsa galimoto iliyonse ndikuchita chipikisheni kubuti. Ati apolisi amaopa kuti anthu ena apita ndi zida kumsonkhano wa PAC [Public Affairs Committee],” adatero iye.

Msonkhano wa bungwe lounikira momwe dziko lino likuyendera la PAC udali kuchitika ku Sunbird Mount Soche ndipo usanayambe mlangizi wa pulezidenti pa zochitika m’dziko muno Hetherwick Ntaba adati boma limadziwa kuti pali anthu 300 amene amakonza zipolowe msonkhano wa PAC ukangotha. Msonkhanowo udaliko Lachitatu ndi Lachinayi.

Ndipo Kumbukani Mhlanga wa ku Chinyonga adati adadabwa kuona apolisi akuimika galimoto iliyonse yolowa m’tauni.

“Zidatichedwetsa ku ntchito. Ndipo ndimadabwa kuti chikuchitika n’chiyani ndisanamve kuti kuli msonkhano wa PAC,” adatero iye.

Kuchuluka kwa apolisi sikudali m’misewu mokha, ngakhalenso kuhotelayo, apolisi adali mbweee, ena atanyamula mfuti zawo. Pa gulu la apolisi omwe anali ku msonkhanowo, oitanidwa ndi PAC adali 6 okha, malinga ndi mkulu wabungwelo Robert Phiri.

Koma Phiri adati kuonjezereka kwa apolisiwo sikunasokoneze dongosolo lawo chifukwa adakonzekera.

“Tidadziwa kuti apolisi abwera ochuluka potengera nkhani zomwe zidamveka za chisokonezo. Mwina nthumwi zina zidasokonezeka, koma ife tachita mmene tidakonzera,” adatero Phiri.

Mmodzi mwa nthumwi ku msonkhanowo, mkulu wa bungwe la People’s Land Organisation (PLO) Vincent Wandale adati anthu adadabwa ndi gululi, koma adamasuka kukamba zotukula dziko.

“Zidali ngati dziko likulamulidwa ndi apolisi. Nthumwi zaboma zidabwera zambiri, sitikudziwa kuti amaopa chiyani. Ubwino wake aliyense adapereka mfundo zimene adakonza.  Zoopa apolisi zidali kale ndipo sitidanjenjemere kupezeka kwawo,” adatero Wandale.

Mneneri wa polisi m’dziko muno James Kadadzera adati kuchuluka kwa apolisi sikudali kuopseza anthu koma kupereka chitetezo.

“Ndife osangalala kuti msonkhano watha popanda zovuta zili zonse. Timapezeka pofunika chitetezo kuti aliyense agwire ntchito yake mosaphwanya lamulo osati kuopseza. Ndipo okonda dziko lake sanganene kuti apolisi adalakwitsa,” adatero Kadadzera.

Chitetezo chapolisi chokhwimachi chidaonekeranso pamene apolisi mogwirizana ndi khonsolo ya mzinda wa Blantyre adaphwanya ndi kulanda makontena amene anthu amachitiramo bizinesi mumzindawo. Izi zidachitika usiku wa Lolemba ndi Lachiwiri.

Related Articles

Back to top button
Translate »