Chichewa

Apumphuntha ana ndi nsimbi

Listen to this article

 

Ana atatu a banja limodzi abwerera lokumbakumba mayi wawo Eveter Kulemera, wa zaka 24, akuti atawalumira mano kuwapumphuntha ndi nsimbi yotchezera mowa wa kachasu m’mudzi mwa Pemba kwa T/A Kachere m’boma la Dedza.

Pakalipano mwana mmodzi, wa zaka ziwiri, ali chigonere mutu uli chitupile m’chipatala cha boma cha Dedza pomwe mbale wake, wa zaka zitatu, akuvutika ndi msana ndipo wina wa zaka zisanu ali nkhasako chifukwa akuti adakwanitsa kuthawa ataona zomwe makeyo amachita.

Gogo wa ana ndi mchemwali wa mayi yemwe  adavulaza ana ake kudwazika matenda m’chipatala cha Dedza Lachinayi
Gogo wa ana ndi mchemwali wa mayi yemwe adavulaza ana ake kudwazika matenda m’chipatala cha Dedza Lachinayi

Gogo wa anawo Catherine Moses, yemwe akudwazika matendawo, adati pa 17 December, khunyu lidagwira mayi wa anawo dzuwa likuswa mtengo ndipo atatsitsimuka adatenga mankhwala onse omwe adalandira kuchipatala n’kumwa ati kuti afe.

Iye adati pambuyo pake adayamba kutukwana anthu pamudzipo uku akunena kuti akufuna afe koma atenga ana ake ngati mitsamiro, koma anthu amaona ngati tchetera poti nthawi zambiri amatero nthendayo ikayamba.

“Poyamba anthu amangoti n’zakhunyu, koma kenako adangomva ana akulira momvetsa chisoni ndipo atathamangirako adakamupeza nsimbi yofululira kachasu ili m’manja akumenya nayo ana akewo,” adatero gogo wa anawo.

Gogo Moses adati anthu achifundo adatengera anawo kuchipatala cha Lobi pomwe ena adapanikiza mayiyo ndi zibakera komanso mitengo koma atawapulumuka, adathawa n’kukadziponya mumtsinje wa Luwenga womwe uli pafupi ndi mudziwo.

Gogoyu adati anthu omwe amathamangira mayiyo adamuvuula n’kumutengera kunyumba koma adakathawanso n’kukadziponyanso mumtsinjewo ndipo anthu odutsa adamuzindikira n’kumuvuulanso ndi kukamuperekeza kwawo.

Monse zimachitika izi, akuti nkuti gogoyu ali kumunda ndipo anthu ena ndiwo adakamuuza kuti adzukulu ake awatengera kuchipatala ndipo adangouyamba kulondola.

“Chichokereni moti ndilibe chithunzithunzi kuti kuli bwanji chifukwa anthu odzandiona kuno akuti chifukwa chokwiya kuti anthu adalanditsa anawo, [mayi wa anawa] adayamba kulimbana ndi nyumba yanga mpaka adagwetsa chipupa chimodzi.

“Akuti sikudali bwino ndipo palibe amayandikirako. Ena adandiuza kuti adatenga musi n’kuyamba kumenya nyumba yanga mpaka kugwetsa chipupa moti sindikudziwa kuti ndikatuluka ndikafikira poti?” adatero gogoyo.

Adotolo pachipatala cha Lobi ataona momwe anawo adalili, akuti adaitanitsa ambulansi kudzawatenga kupita nawo kuchipatala cha Dedza kuti akalandire thandizo msanga.

Namwino, yemwe amayang’anira m’chipinda chogona ana pachipatalapo tsiku lomwe Msangulutso udapitako kukawaona, adati anawo adafika ali chikomokere ndipo wamng’ono zediyo adafikira m’chipinda cha matenda akayakaya.

“Sadali mwakanthu moti tidachita kumuika pa oxygen [makina ampweya] chifukwa amalephera kupuma. Mubongo mukukhala ngati mudakhuthukira magazi moti tikudikira adotolo kuti amuunikenso kuti mwina timutumize kuchipatala chachikulu cha Kamuzu Central,” adatero namwinoyo.

Gogoyo adati mayi wa anawo adayamba kugwa khunyu ali ndi zaka 10 ndipo amuna okwana atatu akhala akupalana naye ubwenzi mpaka kumpatsa ana atatuwo koma amamuthawa akazindikira kuti amagwa khunyu.

“Ana atatu onsewa ndamuthandiza kulera ndine ndipo ndavutika nawo kwabasi moti ndikumva kuwawa kuti iyeyo adaganiza kuchita zimenezi,” adatero gogoyo.

Mkulu wake wa mayi wa anawo, Jennifer Wilson, adati anawo akachira adzawatenga chifukwa chomwe chili kumtima kwa mng’ono wakeyo sichikudziwika.

“Ndilolera kuti ngakhale ndili ndi mavuto anga, iyeyo asadzasungenso anawa, ndidzangowatenga angadzawapange zoopsa kuposa apa chifukwa sitikudziwanso kuti ali ndi malingaliro otani,” adatero Wilson.

Iye adati zitachitika izi, mayi wa anawo adamutengeranso kuchipatala chifukwa adafooka ndi mankhwala omwe adamwawo komanso chifukwa adamenyedwa kwambiri ndi anthu okwiya ndi zomwe adachitazo.

Wilson adati abale ake a mayiyo akufuna kuti achipatala akamuyeze ngati khunyulo lakhodzokera kumisala monga momwe iwo akuganizira.

Mneneri wa polisi m’bomali, Edward Kabango, adati anthu adangotengera ana ndi mayiyo kuchipatala koma osakanena chilichonse kupolisi chifukwa m’mabuku awo a milandu mulibe dandaulo lokhudza nkhaniyi.

“Ndamvera kwa inu ndipo nditafufuza pachipatalapo ndapezadi kuti pali nkhani yotero koma ife sitidalandire ndandaulo lililonse pankhaniyi,” adatero Kabango. n

Related Articles

Back to top button
Translate »