Religion News

Apumuntha Mlaliki kuchipatala cha QECH

Listen to this article

Kudathetheka makofi kuwodi 3B pachipatala cha Queen Elizabeth Central Hospital (QECH) mumzinda wa Blantyre mkulu amene amalalikira uthenga wabwino kuona mbonaona kaamba ka anthu amene adamwalira mokaikitsa.

Wachitetezo wina pachipatalapa, Veronica Zimba, akuti mkuluyu, yemwe dzina lake silikudziwika, adafika kuchipatalako pa 4 April pamene adayamba kulalikira ndi kupempherera odwala. Koma chodabwitsa anthu 6 amene adawapempherera adamwalira tsiku lomwelo iye atangotuluka.

“Tsiku lotsatira [lomwe lidali Loweruka] mkuluyu adabweranso kudzachititsa mapemphero. Tsoka lake adakumana ndi makolo ena amene amayang’anira wodwala ndipo adamwalira, ndiyetu adayamba kutikita,” adatero Zimba.

Zimba adatinso atasunzumira chikwama chomwe mkuluyu adatenga mudali mankhwala achikuda ndi zithumwa komanso zithunzi za njoka zojambulidwa ndi makala.

“Tidamutengera kupolisi ya Blantyre,” adawonjezera.

Mneneri wa polisi ya Blantyre Elizabeth Divala watsimikiza za nkhaniyi koma wati afufuze kaye zenizeni zomwe zidachitika.

“Ndangomvanso kuti kwafika munthu amene wamenyedwa ku QECH koma ndifufuze kaye,” adatero Divala.

Potsimikiza nkhaniyi, mkulu wa chipatalachi, Themba Mhango, adati zidangochitika kuti kamunayu adamukutumula chifukwa panalibe kugwirizana pakati pa pemphero lake ndi kumwalira kwa anthu. Iye sadatsimikize zachiwerengero cha anthu omwe adataya miyoyo yawo patsikulo.

“Zoona amumenya. Koma zangochitika kuti zidatero chifukwa sindikuona kulumikizana kwa kumwalira kwa anthu ndi mapemphero ake,” adatero iye.

Related Articles

Back to top button