Asimba za kasamalidwe ka mpunga

Listen to this article

M’maboma a Nsanje, Chikwawa, Machinga komanso maboma ena kuchigawo cha kumpoto alimi a mpunga ali kalikiriki ndi ulimi wa mpunga wamthirira womwe akhale akukolola mu December muno. Kuti mpunga ulimidwe pali zambiri zomwe zimatsatidwa monga kuthira feteleza mwa zina. BOBBY KABANGO adali kusikimu ya Muona m’boma la Nsanje komwe adacheza ndi Grace Misolo, yemwe walimanso mpunga. Iye akufotokoza momwe alimi angasamalire mpunga wamthirira.rice

Tidziwane, achikumbe…

Ndine Grace Misolo wa m’mudzi mwa Goke kwa T/A Mlolo m’boma lino la Nsanje. Ndine mlimi wa chimanga ndi mpunga komanso ndimachita bizinesi yogulitsa njerwa.

Mukugwira ntchito yanji m’mundamu?

Lero ntchito ilipo ndi kuthira feteleza. Ndabwera mmawa uno kuti ndimalize dera lonse kuti mawa ndiyambe kuzulira.

Mukuthira feteleza wanji?

Ndangosakaniza Urea ndi 23:21:0+4s. Urea ndi wobereketsa pamene winayu ndi wa nthaka.

Mwasakaniza chifukwa chiyani?

Alangizi amatirangiza kuti tiyambe kuthira 23:21:0+4s ndipo timalizire ndi Urea koma ine ndidakanika chifukwa cha mavuto ena. Komabe zikatere si ndiye kuti zavuta, timangodikira kuti mpunga wathu ufike mlingo wabwino n’kuthira feteleza wosakaniza.

Kodi ndondomeko yake imakhala bwanji ya momwe mungathirire feteleza?

Tidaphunzitsidwa kuti, tikangofesa mpunga wathu panazale, feteleza mukhale mwagula kale kuti musavutike. Tikabzala, timadikira padutse masiku 10 ndiye timathira feteleza wa 23:21:0+4s. Tikatero timadikira ndithu kuti padutse masiku 20 pamene timabwera ndi feteleza wa Urea. Kuthira kumeneku kumakhala komaliza ndiye timangoyang’anira uko tikudikira tsiku loti tiyambe kukolola.

Inu mwatsatira ndondomeko iyi chifukwa chiyani?

Chomwe chidachitika n’chakuti ndidadumphitsa kuti ndithire feteleza woyamba patatha masiku 10 ndiye ndidangodikira kuti mpungawu ukangogwirana bwino kufika mlingo uliwu ndithire feteleza wanthaka komanso wobereketsa. Izi zimathekanso ndipo ndakhala ndikuzichita.

Kodi mukamathira feteleza, madziwa mumawachotsa?

Monga mukuonera m’munda mwangamu kuti ndatseka kuti madzi asalowenso ndi cholinga choti pamene ndikuthira feteleza madzi akhale ochepa. Ngati wathira feteleza muli madzi, fetelezayo sagwira ntchito chifukwa amangokokololedwa ndi madziwo.

Kathiridwe kake mumangowaza choncho?

Eetu, mpunga sitibayira monga zichitikira ndi mbewu zina. Timangowaza chonchi ndipo amagwira ntchito bwinobwino.

Munda wanu ndiwokula bwanji?

Sindidayezepo koma ndili ndi mabandi anayi.

Mumakolola wochuluka bwanji?

Uli wa mvula ndidakolola matumba 26 olemera ndi makilogalamu 50 koma wosapuntha. Ulimi wa mthirirawu ndiye ndikuyembekeza kukolola matumba 22. Apapa ndalima mpunga wa taichuni koma nthawi ya mvula ndidalima faya.

Mwapindula bwanji ndi mpunga?

Ndamangitsa nyumba, ndikulipirira ana atatu ku sekondale komanso ndagula ng’ombe zitatu kuchokera mu ulimiwu.

Kodi mumabzala bwanji mpungawu?

Mapando amatalikirana ndi ma sentimita 9 pamene m’litalimu mutalikirane ndi masentimita 6. Paphando timabzalapo mpunga umodzi, aka ndi kalimidwe kamakono kamene alangizi adatiphunzitsa.

Related Articles

Back to top button