Nkhani

Asimbe lokoma ndani?: Civo, Manoma aswana mu Standard Bank

Listen to this article

 

Pali ntchito mawa pabwalo la Civo mumzinda wa Lilongwe pamene timu ya Civo United ichapane ndi Mighty Be Forward Wanderers m’ndime yotsiriza ya chikho cha Standard Bank.

Matimu onse adapatsidwa sabata imodzi yoti akonzekere masewerowa ndipo mawali ndi lomwe amene wotenga chikhochi adziwike. Silver Strikers ndiyo idatenga chikhochi chaka chatha itapuntha Azam Tigers 2-0.

Civo yafika m’ndimeyi kawiri, mu 2009 pamene idakang’anthidwa ndi Tigers kudzera m’mapenote komanso mu 2010 pamene idakhaulitsidwa ndi Moyale kudzeranso m’mapenote.civo

Manager wa Civo, Rashid Ntelera wati palibe chatsopano chomwe timu yawo yakonzera osewera ngati angatenge chikhochi mawa.

“Malamulo athu ali momwe alili. Kupambana masewerowa ndiye kuti tili ndi K10 miliyoni, osewera adzagawana K6 miliyoni yomwe ndi ndalama yambiri, osewera akudziwa kale zoyenera kuchita komanso ubwino wotenga chikhochi,” adatero iye.

Wanderers yatengapo chikhochi kawiri, mu 2012 pamene idaumbudza Silver 2-0. Idachiteteza mu 2013 pokhaulitsanso Silver 1-0.

Manager wa Wanderers Steve Madeira akuti chilichonse chakonzeka kuti mawali alange Civo ndi kutenga chikhochi kachitatu.

“Mukudziwanso kuti Wanderers ikamamenya m’chikho imaikirapo mtima kwambiri. Komanso anyamata akudziwa kuti kungatenga K10 miliyoni ndiye kuti akatamukiratu. Tikudziwa kuti masewerowa akakhala ovuta komabe osapotera nyerere adziwe kuti tikachita zakupsa,” adatero.nomads

Momwe matimuwa ayendera kuti afike m’ndimeyi.

Wanderers ndiyo yasewera masewero ambiri chifukwa idachita kuvoteredwa ndiye idayambira m’ndime ya chipulula pamene idatulutsa Mafco 4-3 kudzera m’mapenote.

M’ndime ya makotafainolo, Civo idachapa Dedza Young Soccer 2-0 pamene Wanderers idathowa Red Lions 1-0.

M’ndime ya semifainolo, Civo idalanga Bullets 2-1 pamene Wanderers idatuwitsa Blue Eagles 1-0. Lero matimu amene akhala akulanga anzawo m’chikhochi akuyenera kulangana.

Muhammad Sulumba akhala wosewera wofunikira kwambiri ku Wanderers chifukwa ndiye waifikitsa timuyi m’ndimeyi atagoletsa chigoli chimodzi pokumana ndi Eagles.n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »