Nkhani

Asintha mlandu wa ‘fisi’

Apolisi Lachinayi adasintha mlandu wa Eric Aniva, amene adamangidwa ataulula kwa mtolankhani wa BBC kuti amagona ndi ana achichepere komanso amayi amasiye potsata miyambo ya makolo. Mneneri wapolisi m’dziko lino Nicholas Gondwa adati adasintha mlanduwo kuchoka pomuganizira kugona ndi ana, kufika ku mlandu woika moyo wa wina kukhala pachiopsezo cha imfa.

Mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adalamula apolisi kugwira Aniva wa zaka 40 atauza atolankhaniwo kuti adagona ndi amayi ndi ana 104 mosadziteteza potsata mwambo wa kusasafumbi—umene umachitika msungwana akatha msinkhu—ndi wa kulowakufa, umene umachitika kwa mkazi wamasiye pofuna kukhazika pansi mzimu wa mwamuna wake.

Adamangidwa: Aniva
Adamangidwa: Aniva

Gondwa adati akumuzenga mlandu woika miyoyo ya ena pachiswe mosemphana ndi ndime 1 komanso 2 za gawo 5 ya malamulo oti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo pantchito. Iye adati adasintha polingalira kuti ngakhale Aniva amadziwa kuti ali ndi kachilombo koyambitsa matenda a Edzi ka HIV, iye amagonabe ndi asungwana ndi amayiwo osawauza.

“Atapezeka wolakwa akhoza kulipa K1 miliyoni kapena kukakhala kundende zaka zisanu akugwira ntchito ya kalavula gaga,” adatero Gondwa.

Mneneriyo adaonjeza kuti padakalipano, Aniva waulula abambo ena amene amagwira ntchito yaufisi, pomwe amalandira K3 500 mpaka K5 000 akagona ndi mayi kapena msungwana.

Aniva, yemwe adakaonekera kukhoti la Nsanje Lachinayi, akusungidwa kundende ya m’bomalo pomwe apolisi akufufuzabe za nkhaniyo.

Polankhula ndi BBC, Aniva akuti adati adayamba ntchitoyi m’zaka za m’ma 1980 ndipo wakhala akugona ndi asungwana a zaka zoyambira 12 komanso amayi amasiye. Iye adauzanso atolankhaniwo kuti amayi ndi asungwana amayamikira ntchito yake. Mkazi wake naye adati amalola amuna ake kugwira ntchitoyo chifukwa amapeza ya mchere.

Koma atafunsa ena mwa amene adagona nawo ali achichepere, adati adavulala ndipo adangolola chifukwa miyambo yawo inkaneneratu kuti ngati salola mwambowo adzadzetsa mlili m’mudzimo.

Koma atamufunsa ngati angalole mwana wake kugonedwa ndi fisi, Aniva adati: “Sindingalole. Ndipo nanenso ndikufuna kusiya ufisiwu.” n

Related Articles

Back to top button