ChichewaEditors Pick

Atentha nyumba kaamba ka K2 000

Listen to this article

 

Mkulu wina ku Ntchisi waona mbwadza atagamulidwa kuti akaseweze zaka 8 kundende kaamba kobutsa nyumba ya mnzake chifukwa cha ngongole ya K2 000.

Bwalo la milandu ku Ntchisi pa 27 November lidalamula Thokozani Paul, wa zaka 21, yemwe amachokera m’mudzi mwa Mdaopamudzi m’dera la T/A Nthondo m’bomali kuti akagwire ntchito yakalavulagaga kaamba koyatsa nyumba ya nyumba ya Winston Njirisi, wa zaka 39.

Fire

Woimira boma pamilandu, Sergeant Austin Daudi, adauza bwaloli kuti bamboyu, yemwe ali pabanja komanso ali ndi ana, adapalamula mlanduwu usiku wa pa 21 November pamudzi wa Chimbaka m’dera la Nthondo lomwelo.

Malingana ndi Daudi, Njirisi akuti adali ndi ngongole ya K2 000 ya womangidwayu yomwe ankafuna kugulira ndowa ya chimanga.

“Wodandaula adalephera kupereka ndowa ya chimanga kwa womangidwawa komanso kubweza K2 000, zomwe zidakwiyitsa omangidwawa.

“Patsikulo onse awiri adapita kukamwa mowa ndipo ali komweko mkangano udabuka kaamba ka ngongoleyo ndipo mkanganowo udakafika mpakana kunyumba ya wodandaulayu,” adatero Daudi.

Iye adati cha m’ma 7 koloko usiku Paul adanyamuka kunyumba ya Njirisi kupita kunyumba kwake ndipo patangodutsa mphindi makumi atatu, adabwerera ndi cholinga chokabutsa nyumba ya mnzakeyo ndipo panthawiyo nkuti Njirisi akugona m’nyumbamo ndi banja lake pomwe nyumbayi imayaka. Adapulumuka kaamba ka kukuwa kwa anthu amene adaona nyumbayo ikuyaka ndipo adathawira panja atangopulumutsamo chitenje chimodzi ndi masikito.

Atakaonekera kukhoti pa 27 November, Paul adapezeka wolakwa pamlandu wotentha nyumba motsutsana ndi gawo 337 la malamulo a dziko lino.

Popereka chigamulo, majisitireti Dorothy Kalua adati mlanduwu ndi waukulu potengera kuti wodandaulayo adamusiya padzuwa popeza nyumba ndi katundu wambiri adapsera momwemo.

Related Articles

Back to top button