Nkhani

Athotha a kabaza opanda mapepala

Listen to this article

Boma lalamula apolisi m’dziko muno kuti athothe akabaza onse a njinga zamoto zopanda mapepala oziyenereza kuyenda pamsewu ndi kumanyamula anthu.

Chikalata chomwe apolisi atulutsa chati boma laganiza izi pofuna kuchepetsa ngozi zomwe zimachitika chifukwa cha akabaza osatha kuyendetsa njinga ya moto komanso njinga zosayenera kuyenda pamsewu.

Njinga za kabaza zawanda kwambiri m’Malawi

Malingana ndi zomwe Tamvani yapeza kupolisi, pakati pa January ndi September 2020, ngozi zokhudza akabanza a njinga zamoto zidakwana 879 ndipo oyendetsa njingazo adamwalirapo anthu 77.

Sitingakhale chete n’kumangoonerera ngozi zopeweka ngati izi zikuchitika. Apapa tayamba kuwathotha makamaka omwe njinga zawo zamoto zilibe mapepala oyenelera.

Tamvani adapezanso kuti njinga 41 zidabedwa mwaupandu ndipo eni ake adavulazidwa kapena kuphedwa polandidwa njingazo.

Koma mmodzi mwa ochita bizinezi ya kabaza wa njinga yamoto Macwilliams Sokotani wati ngakhale zili zoyenera kutero, boma lapupuluma.

Iye wati bomalo likadayamba lakumana ndi ochita bizinezi ya kabazawo n’kukambirana nawo mwinanso kuwaphunzitsa zina zochita uku akuthetsa bizinesiyo pang’onopang’ono.

“Amatero nanga kungoti kamodzi n’kamodzi fyiii? Mesa bwenzi akuchita pang’onopang’ono kuti nafe tipeze mpata wosintha zochita,” watero Sokotani.

Iye wati nyengoyi ndi yanjala ndipo ambiri ochita kabaza amadalira bizinesiyo kuti azidyetsa mabanja awo komanso azitukula miyoyo yawo pachuma.

“Ku Malawi kuno ntchito n’zosowa kale moti ena mwa ochita kabazawa ndi anthu a sukulu zawo koma kusowa chochita ndiye akutiso tichoke, tizikatani tsopano,” watero Sokotani.

Mkuluyu ndi mmodzi mwa ochita kabaza m’tauni ya Lilongwe ndipo wagwirizana ndi mnzake Maurice Hiwa yemwe wati ngati kuli kotero, boma lithamangitse pulogalamu yopezera anthu 1 miliyoni ntchito.

“Mmalo moti azitipezera chochita, agundika kutithirira mchenga m’chakudya. Adatiuza pakampeni kuti adzatipezera ntchito koma kuli zii mmalo mwake ndi awa akufunanso atitsekele m’godi,” adatero Hiwa.

Related Articles

Back to top button