Nkhani

Atibera—Chakwera

Listen to this article

Yemwe adaimira chipani cha MCP, Lazarus Chakwera, dzulo adati sakuvomereza chisankho cha pa 21 May, ponena kuti adaberedwa mavotiwo.

Polankhula kwa atolankhani kulikulu la chipanicho ku Lilongwe, Chakwera adati akugwiritsa ntchito gawo 114, ndime (1) komanso (3) (d) ya malamulo oyendetsera chisankho a dziko lino.

Chakwera: Tikupita kukhoti

“Ine, Lazarus Chakwera, sindikuvomereza zotsatira zachisankho cha pa 21 May. Lidali khumbo langa kuti ndipemphe bwalo la milandu kuti [Peter] Mutharika asalumbiritsidwe koma sindidafune kuti zisokoneze Amalawi, chifukwa ntchito zaboma zikadaima,” adatero iye.

Gawo la malamulo limene Chakwera akugwiritsa ntchitolo limapereka ufulu kwa amene akuona kuti chisankho sichinayende bwino kukasuma ku bwalo lalikulu la milandu.

Chakwera adati madandu ake adagwa pa makutu osamva ku bungwe la zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC).

Iye adadzudzula mchitidwe wa otsatira chipani cha MCP ena amene amachita ziwawa m’madera ena pokwiya ndi zotsatira za chisankho.

“Izi n’zosayenera. Koma tikudandaula kuti ulamuliro wolandawu wayamba kale kuonetsa mawanga ake chifukwa taona ogwira ntchito m’boma, apolisi komanso asilikali akusamusidwa chifukwa akuoneka kuti ndi wotsatira MCP kapena akuchokera pakati ndi kumpoto,” adatero iye.

Mawu a Mutharika adadza bungwe lounikira momwe zinthu zikuyendera m’dziko muno la Public Affairs Committee (PAC) litalengezanso kuti silikukhutira ndi zotsatira za chisankhocho.

Wapampando wa bungwelo, limene limabweretsa pamodzi mipingo yonse m’dziko muno, mbusa Felix Chingota adadzudzula MEC posokonezaa kayendetsedwe kachisankho.

“Poyamba zonse zimayenda bwino koma MEC idayamba kusokoneza makamaka nthawi yolengeza zotsatira za chisankho. Kuvomereza kwa mkulu wa MEC Jane Ansah kuti bungwelo lidavomereza ngakhale zotsatira zimene zidafutidwa zikusonyeza kuti pena padakhota nyani mchira,” adatero Chingota.

Polengeza zisankho, Ansah adati ngakhale bungwe lake silidapereke zofutira zotsatira za zisankho, bungwelo lidalandira zotsatira zofutidwa kuchokera m’madera onse a dziko lino.

Izi zili apo, oyang’anira zisankho ochokera maiko akunja komanso mgwirizano wa mabungwe a zisankho la Malawi Electoral Support Network (Mesn) adavomereza zotsatirazo.

Related Articles

Back to top button