Nkhani

Atsatsidwa kugula anthu kawiri

Listen to this article

Njonda ina yomwe ikuchita bizinesi yake ya golosale ndi chigayo pa boma ku Dowa yadandaula kuti anthu akuiwonongera mbiri chifukwa yatsatsidwapo anthu kawiri konse.

Stanley Ishmael adauza Msangulutso kuti zimenezi ndizongofuna kumuonongera mbiri yake chifukwa iyeyu sagula anthu.

“Anthu akakhala, basi amangoganiza kuti timapanga zimenezo, koma sichoncho. Sindipanga zimenezo,” adatero Ishmael.

Malinga ndi Ishmael, miyezi yapitayo, amayi ena adafika pagolosale yakeyo kukatsatsa amuna awo pomwe sabata yatha mnyamata wina adamutsatsa msuweni wake wa zaka 20 pomutchula kuti nkhuku yoyera.

Ishmael adalongosola kuti adadzidzimuka sabata yathayi ataitanidwa ndi mzake wina kuti kwabwera kalata yake kuchokera kwa mkulu wina wa zaka 26 wochokera m’mudzi mwa Chinyanya T/A Chiwere m’boma la Dowa.

“M’kalatamo adalongosola zoti wakhala akulota katatu konse ndikumufunsa ngati ali ndi nkhuku yoyera,” adalongosola Ishmael.

Iye adati apa awiriwo adamuitanitsa mkuluyo kuti adzawalongosolele zomwe amatanthauza m’kalatamo.

“Apa adatiuza kuti umphawi wamuvuta ndipo ali ndi munthu woti akufuna kundigulitsa. Izi zidandiopsa ndipo ndidakaitula nkhaniyi kupolisi komwe adandiuza zochita,” adatero Ishmael.

Iye adati mkuluyo adamtumiza msuweni wake wa zaka 20 yemwe amamtsatsayo kugolosale ya Ishmael ati kuti akamuone.

Malinga ndi Ishmael, adamuitanitsanso mkuluyo kuti adzalongosole bwino za malondawo.

“Sadachedwe ayi. Adabweradi, apa nkuti nditawauza kale apolisi ndipo apolisiwo adatipeza tikukambirana za mtengo womwe panthawi yomwe amam’mangayi adali asadatchule,” iyer adatero.

Koma Ishmael adati apolisiwo atangofika pamalopo mkuluyo adayamba kukana kuti sichoncho, koma apolisi adamumanga kuti akayankhire komweko.

“Aka nkachiwiri anthu kundipanga zimenezi. Zikundionongera mbiri yanga ngati munthu wa bizinesi. Izi zimandinyansa. Padabweranso mzimai kudzanditsatsa mwamuna wake, nkhaniyi ndidaipititsanso ku polisi,” adatero Ishmael. n

Related Articles

Back to top button