Chichewa

Atsekera wogwiririra Gogo wa zaka 80

Listen to this article

 

Bambo wa zaka 54 yemwe adagwirira gogo wa zaka 80 ku Dowa amulamula kuti akaseweze zaka ziwiri ndi theka atamupeza wolakwa pamlanduwu.

Khoti la Msongandewu, lomwe lili ku Mvera m’bomalo lidapereka chilangocho kwa mkuluyo, Biwi Ephraim wa zaka 54, koma anthu ozingwa ndi zimene adachitazo ati chigamulocho n’chofooka.

Anthu a m’mudzi mwa Nyemba kwa Mfumu Yaikulu Chiwere m’bomalo adaima mitu ndi zomwe Ephraim adachita pogwiririra gogoyo potengera danga kuti gogoyo adaledzera.

Chomwe chaimika mitu anthuwa n’chakuti bamboyu ali pabanja ndipo ali ndi ana 7. Anthu a m’mudzimo ati sakumvetsa chomwe chidamukopa bamboyu kunyazitsa gogoyo.

Mmodzi mwa anthuwo, Joel Machira, adati: “Izi zikachitika, timaganizira masilamusi kapena kukhwima chifukwa munthuyu ali ndi banja ndipo ngati m’thupi munatentha akadatha kupeza mpumulo kunyumba kwake.”

Kaponda: Gogoyo adapita kokamwa

Ndipo Rose Thodwa adati mkuluyo adayenera kulandira chilango chokhwimirapo.

“Uku nkuvula mtundu chifukwa gogo wa zaka 80 ndi mtsitsi wa anthu ambiri ndiye kumupanga chipongwe n’zosamveka,” adatero Thodwa.

Mneneri wa polisi m’bomalo, Richard Kaponda adati patsiku la chipongwelo, gogoyo adapita kukamwa mowa m’mudzi mwa Chiponda m’dera lomwelo ndipo pobwerera, bambo wachipongweyo amamuzemberera.

“Atafika m’mudzi mwa Chifisi, adambwandira gogoyo n’kumukokera patchire pomwe adamuchita chipongwecho ndipo achipatala cha mishoni cha Mvera  adatsimikiza kuti adagwiriridwa,” adatero Kaponda.

Ephraim amamuzenga mlandu wogwiririra zomwe zimatsutsana ndi ndime 132 yamalamulo ndipo iye adakana mlanduwo koma woyimira boma Sergeant Benedicto Mathambo adabweretsa mboni zitatu m’khothimo. Iye adati chilango chokhwimitsitsa chimene akadalandira n’kukhala kundende moyo wake onse.

Wolakwayo adapempha ogamula mlanduwo majisitileti Amulani Phiri kuti amuganizire pogamulapo chifukwa ali ndi banja lofunika chisamaliro komanso ndi wamkulu.

Popereka chigamulocho, Phiri adati zomwe adanena Mathambo nzomveka komanso potengera umboni omwe udaperekedwa m’khotimo, Ephraim akuyenera kukakhala kundende zaka ziwiri ndi theka akugwira ntchito yakalavulagaga.

Ephraim amachokera mmudzi mwa Nyemba mfumu yayikulu Chiwere m’boma la Dowa. n

 

Related Articles

Back to top button
Translate »