Chichewa

Atudzula ziwalo za mwamuna wake

Listen to this article

Pamene nkhanza zambiri zomwe zimachita zimakhakla zochokera kwa abambo kupita kwa amayi, Loveness Nakayuni wa m’mudzi mwa Chapyoka, T/A Mwaulambia m’boma la Chitipa, masiku apitawa adali m’chitolokosi pomuganizira kuti adafinya mwamuna wake kumalo obisika mpaka kutudzula ziwalo.

Mneneri wa polisi m’chigawo cha kumpoto Maurice Chapola adatsimikiza za nkhaniyi pouza Msangulutso kuti mayiyo adali m’manja mwawo kaamba kovulaza mwamuna wake, Winis Kita, wa zaka 46, atamugwira kumoyo chifukwa akuti adaphwanya lonjezo logona kunyumba kwake.

Iye adati Kita, yemwe ndi wamitala, adanyamuka kupita kukamwa mowa komwe adabwerako madzulo.

“Iye adafikira kunyumba kwa mkazi wake woyamba, Nakayuni, koma sadakhalitse ndipo adapita kunyumba ya mkazi wake wamng’ono. Izi zidamuwawa Nakayuni, yemwe adamulondola mwamunayo kunyumba kwa mkazi wake wamng’onoyo.

“Atafika adapeza mwamunayo atakhala pakhonde akusuta fodya. Nakayuni adangombwandira malo obisika a mwamuna wakeyo n’kufinya mpaka kutudzula,” adafotokoza Chapola.

Iye adati Kita adamutengera kuchipatala cha boma komwe adalandira thandizo lobwezeretsa ziwalozo zake m’chimake. Pano akuti akupezako bwino ndipo akuchita kuyendera kukalandira mankhwala kuchipatala.

Funso n’kumati kodi banja lilipobe apa?

Tidalephera kuyankhula ndi Kita, koma wapolisi wa zofufuzafufuza, teketivu Yatamu Kasambara, adauza Msangulutso kuti mkuluyu adakatseketsa mlandu kupolisiko ponena kuti zidali zam’banja ndipo mkazi wake pano ali kunyumba ati azikalera ana.

Ku Chitipa komweko, mayi wina, Mawazo Nzunga, akumuganizira kuti wapha mlamu wake atamumenya ndi mpini wa khasu pamutu atalephera kumvetsetsana pankhani ya chakudya.

Chapola adauza Msangulutso kuti wophedwayo, Willard Mwilenga, adapita komwa mowa ndipo pochoka kumowako adaganiza zokapempha chakudya kunyumba ya mbale wake komwe adauzidwa kuti chakudya chake kulibe.

“Yankho la mlamu wakeyo silidamusangalatse ndipo kaamba ka kuledzera adayamba kummenya. Nzunga pobwezera adatenga mpini wa khasu ndipo adamugogoda nawo pamutu n’kumukomola nawo,” adafotokoza Chapola.

Mwilenga adathamangira naye kuchitapatala cha Kameme koma ataona kuti zawakulira adamutumiza kuchipatala chachikulu ku Chitipa komwe adakafera.

Chapola adati Nzunga ali pa rimandi pandende ya Chitipa kudikira kuyankha mlandu wa kupha munthu.

Pothirapo ndemanga pankhani za nkhanza, wapampando wa bungwe la NGO Gender Coordination Network, Emma Kaliya, wati nkhani kuti itengedwe kuti ndi ya nkhaza kwa amayi kapena abambo zimakhala bwino kuyang’ana chatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke m’nyanga.

“M’boma la Chitipa amuna ndi azikazi awo ali ndi kachisimo kokamwa mowa ku ‘chilabu’ limodzi, makamaka madera a kwa Kameme ndi Mwaulambia.

“Tikuyesetsa kuthana ndi mchitidwe womwa mowa ku ‘chilabu’ chifukwa tikukhulupirira kuti umakolezera nkhaza pakati pa amayi ndi abambo,” adatero Kaliya.

‘Chilabu’ ndi malo ogulitsirako mowa, maka wamasese ndi kachasu. n

Related Articles

Back to top button