Chichewa

Atukuka ndi kukwatitsa mitengo ya zipatso

 

Masiku ano nkhani ili mkamwamkamwa paulimi ndi yogwiritsa ntchito mitundu ya mbewu zamakono zomwe akatswiri adayesa n’kupeza kuti zili ndi kuthekera kotukula ulimi. Alimi a zipatso nawo adayambapo kutsata nzeruzi ndipo ena akusimba lokoma. Alimi a gulu la Taweni Farmers Club ku Mzimba akuchita nawo ulimiwu ndipo akudalira kwambiri kukwatitsa mitengo ya zipatso. Wapampando wa gululi Jester Kalua adafotokozera STEVEN PEMBAMOYO za ulimiwu motere:

Mlimi pantchito yake: Kalua kukwatitsa mitengo ya zipatso
Mlimi pantchito yake: Kalua kukwatitsa mitengo ya zipatso

Bambo, dzina ndani?

Dzina langa ndi Jester Kalua wa mmudzi mwa Kamanga kwa T/A Mtwalo ku Mzimba. Ndine wapampando wa gulu la alimi la Taweni Farmers Club.

 

Kodi kalabu imeneyi mumapanga zotani?

Ife timapanga ulimi wa zipatso zosiyanasiyana monga malalanje, mapapaya, mango, mapichesi ndi mapeyala. Tili ndi malo aakulu kwambiri omwe timabzalapo mitengo yazipatsoyi ndipo timathandizana kusamalira ngati gulu.

Inu mumabzala mitundu yotani ya zipatsozo?

Pali ntchito ndithu chifukwa sitimangofesa basi n’kumayembekezera kuti tidzaokere, ayi. Pali zambiri zomwe timachita koma kwakukulu n’kukwatitsa mitengo yathu yazipatso.

 

Mukutanthauzanji mukatero?

Ndikutanthauza kuti timatha kufesa mitengo ina yomwe sivuta kumera n’kusamala panazale koma kenako timaikwatitsa ndi mitengo ina yomwe imabereka bwino koma imavuta kafesedwe kake.

 

Kukwatitsako mumtani?

Tikafesa mitengo yathu timayang’anira mpaka itafika pamsinkhu wokwatitsa. Pokwatitsapo timadula nthambi ya mtengo womwe tikufuna kuti ukwatidwewo n’kuikapo nthambi ya mtengo womwe tikufuna nkumanga. Tikatero timapitiriza kusamalira.

 

Ndiye mtengowo sungafe?

Ayi. Zomwe timachita n’zakuti sitidula nthambi zonse koma mwina imodzi n’kusiya nthambi zina zoti zizipanga chakudya cha mtengowo uku ukugwirana ndi unzakewo. Zikagwirana bwinobwino timatha kudzadula nthambi zinazo kuti mtengo wokhawo womwe tikufuna upitirire kukula.

Cholinga chake nchiyani?

Timafuna kupeza phindu lochuluka paulimi wathu chifukwa mbewu yomwe timaphayo imakhala yobereka pang’ono kusiyana ndi mbewu yokwatitsayo ndiye timafuna kupindulapo pa mbewu inayo.

 

Mungatchuleko mitundu ya mbewu zomwe mukukwatitsa pakalipano?

Tikukwatitsa mandimu ndi malalanje, mango achikuda ndi achizungu komanso mapichesi achikuda ndi achizungu.

 

Ndiye mwati kusiyana kwake nkotani?

Kusiyana kwake nkwakuti mbewu zachizunguzi zimabereka zipatso zikuluzikulu komanso zimabereka kwambiri kuposa mbewu zachikuda.

 

Koma sindikumvetsa pakakwatitsidwe ka mandimu ndi malalanje. N’chifukwa chiyani mumapha mandimu kuti mudzakolole malalanje?

Pali zifukwa zingapo. Choyamba mandimu savuta kafesedwe kake poyerekeza ndi malalanje ndiye timafuna kuti mandimuwo atiyambire moyo wosavutawo kenako n’kuupatsira ku malalanje. Chachiwiri, mandimu ndi malalanje chili ndi msika waukulu ndi malalanje ndiye munthu aliyense akamabzala mbewu zodzagulitsa amaganizira za msika choncho ife timaona chanzeru kulimbikira malalanjewo.

 

Mwanenapo za kasamalidwe, kodi mumasamala bwanji mitengi yanuyo?

Zoonadi mitengo imafunika chisamaliro chokwanira bwino chifukwa kupanda kutero simungapeze phindu. Chiopsezo chachikulu ndi moto wolusa womwe umayamba mosadziwika bwino choncho mpofunika kulambula bwinobwino munkhalango ya zipatso. Kupatula apo mitengo sichedwa kugwidwa ndi matenda osiyanasiyana choncho pamafunika kuyendera pafupipafupi kuti ngati mwaoneka chizindikiro cha matenda, vutolo lithetsedweretu.

 

Nthawi yokolola mumatani?

Choyamba sitingokolola chisawawa koma pamakhala nthawi yake yokololera ndipo timayamba taona ngati zipatsozo zafika poti tikhoza kukolola. Timakana kungokolola chisawawa chifukwa zipatso zokolola zanthete zimabweretsa maluzi chifukwa maonekedwe ake zikapsa amakhala osapatsa chikoka.

Inu misika yanu ili kuti?

Tili ndi misika yosiyanasiyana ya zipatso. Zipatso zina timapikulitsa kwa mavenda ndipo zina timapita nazo m’magolosale akuluakulu omwe amatigulitsira nkumatipatsa ndalama.

 

Mudasankha kulima pagulu basi?

Ayi, timalimbikitsananso kuti aliyense azilima zipatso kumunda kwake kuti azidya pakhomo komanso timalola mlimi yemwe ali ndi zipatso zambiri kubwera nazo kuti timugulitsire tikamagulitsa zipatso za pagulu.n

Related Articles

Back to top button