Chichewa

‘Auka’ atatha zaka 11 m’manda ku ntchisi

 

Pa 16 April 2005 lidali tsiku lachisoni m’mudzi mwa Ngwanje, T/A Malenga m’boma la Ntchisi pomwe mayi Nkomanyama Charles adamwalira akubereka mwana wake wa nambala 6.

Zaka 11 chichitikireni izi, zodabwitsa zaoneka m’mudzimo pomwe munthu amene akumuganizira kuti ndi malemuyo adapezeka ali zungulizunguli mmphepete mwa phiri la Katsumbi mawa wa pa 13 February ali moyo.

Mneneri wa apolisi m’bomalo Gladson M’bumpha, watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati pano mayiyo ali kwa amene akuti ndi makolo ake.

Anthu akukhamukira ku Ntchisi kukaona Nkomanyama
Anthu akukhamukira ku Ntchisi kukaona Nkomanyama

Malinga ndi M’bumpha, apolisi adali amkhalapakati wa zokambirana pakati pa mafumu ndi makolo a mayiyo kuti amulandire.

“Poyamba mayi ake omwe ndi a m’mudzi mwa Chithonje ankachita naye mantha moti ankasungidwa ndi mfumu Katipwiri kufikira titamaliza zokambirana pa 15 February,” adatero M’bumpha.

Mayiyo atangopezeka, yemwe akuti ndi mwamuna wake, Yobu Gwaza, wa m’mudzi mwa Ngwanje, ndiye adayamba kumuzindikira ndipo adafotokoza kuti mkazi wakeyo adamwalira m’chaka cha 2005 akubereka Dorica, mwana wawo womaliza yemwe ali moyobe mpaka pano.

Iye adati adalera yekha mwanayo ndipo chithunzithunzi cha mkazi wakeyo chidali chikadali m’mutu n’chifukwa chake sadachedwe kumuzindikira atamuona.

Gwaza adati alibe vuto lililonse ndi mkazi wakeyo ndipo ndi wokonzeka kumulandira akapeza thandizo nkubwerera munzeru zake bwinobwino.

“Ngati angachire nkukhala bwinobwino chomuletsera kubwerera pakhomo pake n’chiyani? Mmesa ana ake ali kunyumba komweko?” adatero Gwaza.

Anthu akukhamukira kukaona zozizwitsazo, ye,we akuti ndi malume a mayiyo, Masaiti Kalulu, atabweretsa chithunzi chomwe Nkomanyama adajambulitsa asadafe ndipo anthu omwe adachiona kuphatikizapo apolisi akuti pali kufanana pakati pa nkhope ya pachithunziyo ndi mayiyo.

M’bumpha adati anthuwo ataona chithunzicho adakwiya ndi kukana kwa mayi a woukayo ndipo pamalopo padayamba phokoso lomwe adakaletsa ndi apolisi.

“Padali chisokonezo moti chipanda apolisi kufika msanga, pakadachitika chachikulu mwinanso mpaka mayiyo akadamenyedwa,” adatero. Padakalipano mayi akumuganizira kuti adaukayo ali kwa mayi ake koma akuti sakutha kuyankhula komanso nthawi zina amadya mwachidodo.

“Tikukhala naye bwinobwino ngakhale kuti pena amachita zinthu mwachidodo monga kudya. Akhoza kuyamba pano koma kuti amalize pakumatenga nthawi.

“Vuto lina lomwe lilipo ndi losatha kuyankhula ndiye n’zovuta kudziwa chomwe akufuna. Tiona kuti akhala bwanji tikayenda naye,” adatero mayi Charles.

Mfumu Chithonje ya m’mudzi momwe mumachokeratu makolo a mayiyo idatsimikiza za maliro a mayiyo ponena kuti ngoziyo itachita m’chaka cha 2005, idalandira uthenga ndipo idachita nawo mwambo wa malirowo.

Mfumuyo idati kawirikawiri nkhani zokhudza munthu womwalira nkupezeka ali moyo zimazunguza mutu ndiponso zimayambitsa phokoso anthu akazitengera pamgong’o.

Pakalipano apolisi alangiza mafumu ozungulira derali kuti aphe tsiku kupita kukanda kuti akatsimikize ngatidi m’manda momwe adaika mtembo wa Nkomanyama Charles mulibedi thpi lake.

Mkulu wina wa mpingo wa Church of Christ m’boma la Nkhotakota, Maxwel Nangunde, adati amakhulupirira kuti munthu akamwalira basi kwake kwatha mpaka patsiku la chiweruzo.

“Zina ukamva abale koma mpovuta kunena kuti chenicheni nchiti chifukwa anthufe timakhulupirira kuti munthu akapita wapita basi mpaka tsiku la chiweruzo,” adatero Nangunde.

Koma m’mbiri ya chilengedwe tikumva za kuuka kwa akufa kwa Yesu Khristu amenenso adaukitsapo anthu angapo monga Lazalo, mwana wa Jairus kudzanso mnyamata wina wa mayi wamasiye ku Nain.

Tikumvanso kuti pamene Yesu adapachikidwa pamtanda, adaukanso patapita masiku anayi ndipo adalowa m’limbo naukitsa matupi a anthu abwino omwe adafa.

Komanso m’buku la chipangano chakale tikuwerenga za mmene mneneri Eliya adaukitsira mwana wa namfedwa wa Zarephath; Elisha naye adaukitsa mwana wa mkazi wina Mshunammite kwa akufa.

Naye Paulo akuti adaukitsikwa kwa akufa atagedendwa ndi miyala ndi anthu a ku Antioch ndi Iconium n’kumusiya ali thapsa! Komanso Paulo yemwenso akuti adaukitsa Eutychus yemwe adafa atagwa pansi kuchokera panyumba yosanjikizana mmene ankatsinza.

Petulo nayenso adaukitsa mayi wa ntchito zabwino dzina lake Tabitha wa ku Joppa, yemwe amatchedwanso kuti Dorcas, atamwalira n’kuikidwa m’manda.

Izi ndi zina mwa zitsanzo za anthu akufa omwe adaukapo kwa akufa kalelo koma masiku ano anthu ambiri sakhulupirira kuti munthu akafa zenizeni atha kuukanso ndi moyo ndipo palibe umboni weniweni wotsimikiza kuti mayi amene akuti adauka ku Ntchisiyu ndi amene adamwaliradi ndi kuikidwa m’manda pa 16 April 2005. n

Related Articles

Back to top button