Nthawi ikamathamangira 5 koloko mmawa, anthu achipembedzo cha Chisilamu amadzutsidwa kuti akachite mapemphero kumzikiti pamene shehe kapena mwazini (muezzin) amakhala akukuwa.
Koma zachitika ku Nkhotakota si ndizo komwe anthu achiwembu avulaza shehe amene amaitanira mapempherowo.
Mneneri wa polisi ya Nkhotakota, Williams Kaponda, wati izi zidachitika mmawa wa Lachitatu lapitali ndipo sheheyu adamugoneka m’chipatala cha Nkhotakota.
Kaponda adati sheheyu dzina lake ndi Namandwa Ainani, wa zaka 57, amene akuchokera m’mudzi mwa Malenga kwa Senior Chief Malengachanzi m’bomalo.
“Ainani adadzuka mmawa pamene amamemeza anthu achipembedzo cha Chisilamu kuti adzuke akapemphere kumzikiti wa Malenga.
“Iye ankakuwa kuitanira Asilamu kumapemphero ammawa pachikwezamawu, koma ali mkati mochita izi kumzikitiko, achiwembu amene adatenga zida adabwera n’kumuvulaza mkuluyu moti ndikulankhulamu ali kuchipatala cha mishoni cha St. Anne’s,” adatsimikiza Kaponda Lachitatu, koma adati apolisi sakudziwa gwero la chiwembucho ndipo akufufuza kuti apeze ndi kukhwidzinga unyolo amene adachita izi. n