Chichewa

Awiri afa ndi bibida ku KK

Listen to this article

Abambo awiri amwalira ndi mowa wa kachaso m’njira zofanana koma malo osiyana m’boma la Nkhotakota.

Mneneri wa polisi m’bomali, Williams Kaponda, wauza Msangulutso kuti Mphatso Chinguwo, wa zaka 30, adagwa n’kumwalira pamalo ake ogwirira ntchito atalenguka ndi kachaso, pomwe Khiri Bwalo, wa zaka 29, adagwera mchitsime akuchokera komwa kachaso.

Kutcheza kachasu: Mowawu umalengula kupanda kuudyera
Kutcheza kachasu: Mowawu umalengula kupanda kuudyera

“Nkhani zonsezi zachitikadi koma malo ake ndi nthawi n’zosiyana ngakhale kuti onse adamwalira chifukwa chomwa kwambiri kachaso osadyera ndipo Chinguwo adalenguka kwambiri kaamba koti amakakamira kugwira ntchito,” adatero Kaponda.

Iye adati Chinguwo amagwira ntchito yopopa mapaipi otsekeka ndi mnzake Alfred Green, wa zaka 32, m’mudzi mwa Mng’oma kwa T/A Mwadzama m’bomali ndipo Lachinayi, ali mkati mogwira ntchitoyo iye adangogwa, osaphuphaso.

Kaponda adati mnzakeyo ataona izi adagwidwa tsembwe ndipo adathamanga kukaitana anthu ndipo adakafika naye kuchipatala atamwalira kale koma monga mwa mwambo, apolisi adapempha achipatala kuti ayese mtembowo nkuwona chomwe chidamupha ndipo adapeza kuti kudali kulenguka ndi kachaso.

“Timakana kuti pazikhala maphokoso munthu ataikidwa kale poganizirana kuti mwina womwalirayo adachita kuphedwa koma zotsatira zidasonyeza kuti adamwa mowa wa kachaso wambiri osadyera kanthu ndiye adalenguka nawo,” adatero Kaponda.

Iye adatiso Bwalo, wa m’mudzi mwa Tchale, T/A Mwansambo, adalawira bambo ake, Gibson Bwalo, a zaka 63, kuti akukamwa kachaso ndipo pobwererako usiku wa pa 27-28 March adagwera m’chitsime.

“Pa 27 March adanyamuka m’ma 6 koloko madzulo wa kukachaso m’mudzi mwawo momwemo ndipo adapezeka m’chitsime m’ma 6 koloko mmawa wa pa 28 March. Uyuso atamuyesa, adapeza kuti adatsamwa ndi madzi mchitsime momwe adagweramo koma kadali kaamba koledzera ngati woyamba uja,” adatero Kaponda.

 

Related Articles

Back to top button