Nkhani

Ayamba kugawa makuponi

Nduna ya malimidwe Joseph Mwanamvekha yapempha alimi kuti asagulitse makuponi awo amene boma lidayamba kupereka Lachinayi.

Ndunayo idakhazikitsa ntchito yopereka makuponi 4 miliyoni kwa alimi 1 miliyoni ogulira mbewu ndi feteleza pasukulu ya Mtaya m’boma la Balaka.

Nduna ya malimidwe Joseph Mwanamvekha adalangizanso mafumu ndi ena okhudzidwa ndi kugawa makuponi kuti apewe kuba ndi chinyengo pantchitoyi monga zakhala zikukhalira mmbuyomu.

“Ndikunena pano, anthu 58 amene adagwidwa pamilandu ya makuponi chaka chatha. Amene ayerekeze kuba makuponi, lamulo lidzagwira ntchito,” adatero Mwanamvekha.

Iye adapempha alimi kuti ayambe kukonza m’minda yawo kuti azabzale ndi mvula yoyamba chifukwa feteleza afika kumadera m’nthawi yake.

“Chaka chino, makampani amene akugulitsa mbewu ndi feteleza m’maboma onse atitsimikizira kuti afika m’nthawi yake m’madera onse. Tikufuna anthu akangolandira makuponi, nthawi yomweyo agule zipangizo,” adatero Mwanamvekha.

Mmbuyomu, alimi akhala akudandaula chifukwa makuponi amawaolera m’manja kaamba kosowa kokagula zipangizo zotsika mtengo.

Phungu wa dera la kummawa cha pakati m’bomalo Yaumi Mpaweni adapempha alimi kuti agwiritse ntchito makuponi amene alandire.

“Si bwino kugulitsa makuponi anu chifukwa uko ndi kudzipha. Kuti mukolole zokwanira, ndi bwino kuwagwiritsa bwino ntchito,” adatero Mpaweni.

Mwa zina, chaka chino kuponi iliyonse izikhala ndi nkhope ya woyenera kulandira ndi cholinga choti munthu wina asagwiritse ntchito.

Makuponi 4 miliyoni ogulira zipangizo zotsika mtengo adafika m’dziko muno mwezi watha ndipo aperekedwa kwa alimi 1 miliyoni m’chilinganizochi chaka chino.

M’ndondomeko ya zachuma ya chaka chino mpaka chaka chamawa, boma lidapereka K151 biliyoni ku unduna wa malimidwe ndipo K42 biliyoni ipita ku ntchito ya makuponi.

Related Articles

Back to top button