Nkhani

Azula chamba, achiyatsa ku KK

Nkhani zoti apolisi alanda kapena azula chamba ndi zina zokhudza mbewu yozunguzayi sizikukata m’boma la Nkhotakota.

Lachiwiri sabata ino apolisi m’bomalo, mogwirizana ndi asirikali oyan’ganira nkhalango ndi malo osungirako nyama zakutchire adazula chamba m’munda wamaekala atatu.chamba

Izi zachitika apolisi pa 12 September ataotchanso matani 4.5 a chamba amene adalanda kwa njonda zina.

Aka n’ka chi 48 nkhani za mtunduwu kuchitika m’bomalo chiyambireni January chaka chino, apolisi atero.

Mneneri wa polisi m’bomalo, Williams Kaponda, adati munda womwe adazula chambachi uli pakati pa midzi ya Senior Chief Mwadzama ndi T/A Mwansambo.

“Tidapeza chamba chochuluka m’mundawu ndipo tidachizula ndi kuchiyatsa. Kufikira lero [Lachiwiri] palibe amene wanjatidwa pa nkhaniyi, koma apolisi tikufufuza kuti tipeze mwini mundawu,” adatero Kaponda.

“Izi sikuti timapanga tokha, tidali ndi mboni zina monga akuluakulu a bwalo la milandu, khonsolo ya Nkhotakota, achipembedzo, atolankhani, a ku Parks and Wildlife Game Reserve ndi ena.”

Malinga ndi Kaponda, minda ina ya chamba yapezeka m’midzi ya Mwalawamphasa ndi Kanjedza m’boma lomweli. Monga mwa mwambi woti ‘moto umapita kumene kwatsala tchire’, mmeneri wa polisiyu akuti mindayi nayonso aibutsa posachedwapa.

Nkhanizi zikudza pamene pali mtsutso ngati kuli koyenera kuti dziko lino livomereze chamba kuti anthu azilima komanso kugulitsa. M’dziko muno chamba n’choletseddwa kkaamba koti chimazunguza ubongo.

Boma la Nkhotakota limatchuka kwambiri ndi nkhani za chamba, chomwe anthu amalima mobisa m’minda ya chinangwa, nzimbe ndi chimanga.

Related Articles

One Comment

  1. Zitsiru inu muzafa osauka kuotcha chamba zoona,mukufuna kusangalatsa ndani pootcha chambacho. Mwaotchanso ma ivory worth billions of kwacha,why cant u sell them ndikupeza ndalama zogulira mankhwala? It was just amatter of signory btwn we and the buyer and later kumuza kuti tapanga izi just to get lid of this ivory.

Back to top button