Nkhani

Bajeti yadutsa, koma m’zikhomo

Listen to this article

Nyumba ya Malamulo Lachitatu idavomereza bajeti ya K2.2 triliyoni ya chaka cha 2020 mpaka 2021 aphunguwo atayikambirana kuyambira Lolemba.

Bajetiyo yakwera kuchoka pa K1.7 triliyoni mu 2019 mpaka 2020 ndipo ndi bajeti yoyamba ya boma latsopano la Tonse Alliance lomwe akutsogolera Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wake Saulos Chilima.

Adayembekezera zokhoma: Mlusu

Nduna ya zachuma Felix Mlusu adalengeza bajetiyo sabata 5 zapitazo ndipo aphungu adali ndi sabata ziwiri zounika bajetiyo m’makomiti asadayambe kupereka maganizo awo.

Popereka maganizo awo, aphungu osiyanasiyana adaunikira magawo omwe bajetiyo sitidaganizire mokwanira ndipo adapempha Mlusu kuti alingalile magawowo.

Ambiri mwa aphunguwo omwe adali makamaka a mbali yotsutsa adaunikira Mlusu kuti aonjezere ndalama ku maunduna ndi nthambi zina za boma.

Zina mwa nthambizo ndi Nyumba ya Boma, ofesi ya Pulezidenti ndi nduna zake, ofesi yolondoloza momwe ndalama za boma zikugwirira ntchito, unduna woona zoti pasamakhale kusiyana pakati pa amayi ndi abambo komanso chitukuko ndi maunduna komanso nthambi zina.

Phungu wa kummwera m’boma la Chitipa Werani Chilenga adadabwa kuti Mlusu samaonetsa chidwi chofuna kuonjezera zomwe aphunguwo amanena m’bajeti.

Chilenga adati: “Kodi nduna ya zachuma ikufuna tizingovomera zonse zomwe zili m’bajeti? Nanga bwanji sakusintha kalikonse? Ngati akufuna kuti tingovomera bajeti popanda kuunikira atiuze tikhoza kupanga zimenezo lero lomwe.”

Mlusu adavomeleza kuti aphunguwo adamufinya kwambiri pa nkhani ya ndalama zopita m’maunduna ndi nthambi zosiyanasiyana za boma.

“Ndimayembekezera kufinyidwa koma ndidalimba nazo kuwakumbutsa aphungu za komwe tikuchoka ndi momwe thumba lathu lilili. Ndawatsimikizira kuti tiziunika zinthu pang’onopang’ono malingana ndi mmene tizipezera,” adatero Mlusu.

Polankhula mmalo mwa chipani chachikulu chotsutsa cha Democratic Progressive (DPP) Joseph Mwanamvekha yemwe adali nduna ya zachuma m’boma la chipanicho adasambwadza bajetiyo kuti ndi ya njenjete yongodya yosalabadira chitukuko.

“Mukaunika bajetiyo mofatsa, muona kuti siikukhudza kwambiri zotukula ntchito za malonda ngakhale kuti timayenera kuika mtima ku malondako potengera momwe ntchitozo zalowera pansi ndi Covid,” adatero Mwanamvekha.

Mu bajetiyo, boma lakonza zoti K1.679 triliyoni igwire ntchito za malipiro a ogwira ntchito m’boma, kuthandizira nthambi za boma zomwe zimalandira thandizo kuchoka kuboma, kulipira chiongola dzanja cha ngongole za boma ndi ntchito zina zotumikira anthu.

Malingana ndi bajetiyo, K511.2 biliyoni ndiyo yaikidwa kuti igwire ntchito zachitukuko ndipo mwa ndalamazo, K410.3 biliyoni ndi yazitukuko zodalira ndalama zakunja pomwe zitukuko zodalira ndalama za misonkho zalandira K100.9 biliyoni.

Mwa zinthu zikuluzikulu zomwe Amalawi ena anyadira m’bajetiyo ndi kukwera kwa ndalama yoyambira kudula msonkho kufika pa K100 000, kukwera kwa ndalama yoyambira malipiro kufika pa K50 000 komanso pulogalamu ya zipangizo zotsika mtengo yomwe mabanja 4.3 miliyoni azigula feteleza pamtengo wa K4 495.

Related Articles

Back to top button
Translate »