Banja likuganiziridwa kupha mwana wawo

Listen to this article

Apolisi ku Zomba atsekera banja lina poliganizira kuti lidapha mwana wawo wa zaka ziwiri mu January chaka chino.

Mneneri wa apolisi ku Zomba, Patricia Sipiliyano, adati banjali lidachita izi kaamba koti mwanayo, Evance Joseph, adataya mafuta womwe bambo ake womupeza amachitira bizinesi yokazinga tchipisi pa 3 Miles m’bomalo.

Wojambula wathu kufanizira momwe zimakhalira munthu akapalamula mlandu

Sipiliyano adati bamboyu, Peter Kaopya, wa zaka 28 adakwiya kwambiri mwanayo atataya mafutawo moti adamukakha kuchokera pa khonde n’kugwera pansi mpaka kukomoka.

Izi zitachitika mkazi wake, Esther Jonas, wa zaka 22 sadathamangire ndi mwanayo ku chipatala, m’malo mwake adangomutsekera ku chipinda.

Kaopya adali bambo womupeza a Evance pamene Jonas adali mayi ake womubereka.

“Papita maola anayi banjali lidapeza mwanayo atamwalira ndipo lidatenga mtembo wake ndikukaukwirira m’munda wa chimanga.

“Anthu akawafunsa, amayankha kuti mwanayo adamutumiza kwa agogo ake ku Mulanje,” adatero Sipiliyano.

Nkhaniyi yadziwika kaamba koti Jonas adakangana ndi mwamuna wake mpaka kuthamangitsidwa.

Atakafika ku mudzi kwawo ku Mulanje, anthu anamufunsa komwe adasiya mwanayo koma adalephera kufotokoza.

Atamupanikiza, adaulula kuti adamwalira mwamuna wake atamukankha ndipo adamukwirira m’munda wa chimanga.

Jonas adayesa kumwa mankhwala kuti adziphe, koma sizidatheke kaamba koti anthu adathamangira naye ku chipatala msanga.

Apolisi akuimba banjali mlandu wakupha, kubisa imfa, komanso kusunga mtembo m’nyumba.

Kuphatikiza apo, Jonas akuimbidwanso mlandu wofuna kudzipha.

“Tikufufuzabe kuti tidziwe zolinga zenizeni za banjali popha mwana wawo, komanso kukamukwirira m’munda anthu osadziwa,” adatero Sipiliyano.

Kaopya amachokera m’mudzi mwa Sanjika, Mfumu Kwataine, m’boma la Ntcheu pamene Jonas amachokera m’mudzi mwa Kamoto, Mfumu Mkanda, m’boma la Mulanje.

Izi zachitika patangodutsa sabata imodzi bambo wina ku Dedza atamutsekera mchitokosi cha apolisi pomuganizira kuti adaphanso mwana wake womupeza wa zaka zitatu pomupotokola khosi chifukwa choti adabadwa ndi ulumali.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi m’boma la Dedza, Cassim Manda, adati Harrison Kachingwe wa zaka 29 akumuganizira kuti adapha mwanayo mayi ake atapita kukachita bizinesi pa msika wa Golomoti ku Ntcheu.

Related Articles

Back to top button
Translate »