Chichewa

Banki ya m’mudzi yadzetsa udani

Listen to this article

Banki ya m’mudzi yadzetsa udani
Tili ndi gulu lathu la banki ya m’mudzi. Poyamba tidali anthu ochepa koma pano tidachulukana. Timakumana pakhomo la mayi wina ndipo pano adadzipatsa yekha utcheya, ndi mlembi komanso msungichuma. Pano akunena kuti gululi tikamayambiranso tizipereka ndalama yapadera chifukwa amavutika kutilemba m’mabuku. Kodi zimatero?
BC,
Chilumba.

BC,
Ayi ndithu zisamatero. Munthu mmodzi maudindo onsewo chifukwa chiyani? Bwanji mukumupatsa mphamvu zonsezo? Nchifukwa chaketu akukutolani mpaka muzilipira ndalama yapamwamba. Muyenera kugwirizana ndi anzanu ena kuti musankhe anthu okhala m’maudindo kuyendetsa gulu lanu. Komanso simuyenera kukumana pakhomo la munthu mmodzi, muzisinthasintha.

Gogo wanga,
Banja langa lidatha 2013 ndipo mwamunayo adakwatira, nanenso ndidakwatiwa. Vuto ndi lakuti tikakumana, amandinena kuti ndifera zomwezo ndipo tikakhala limodzi ndi mwamuna wanga amafuna mpaka kuwagunda. Ndichitenji?
FC,
Zomba.

FC,
Apa mpofunika kumulankhula amvetsetse bwino lomwe kuti banja lanu lidatha basi iye alibenso gawo pa moyo wanu. Muyenera kuchita zotheka zonse kuti mumuuze kuti zomwe akuchita zikhoza kukusokonezerani banja. Kupanda kumuuza mvemvemve, apitiriza kuchita khalidwe lake lokolalo. Nzovuta kuti ndikuuzeni kuti musinthe njira chifukwa ndi ufulu wanu kudutsa paliponse komanso nkutheka mukhoza kukumanabe.

Zikomo gogo,
Ndakhala paubwenzi ndi mwamuna uyu kwa zaka zitatu. Ndidamuberekera mwana. Vuto lilipo ndi lakuti tikamaseleulana, amakonda kundinena kuti ndine wosaoneka bwino, zomwe zimandikhumudwitsa. Polingalira kuti nthawi zambiri munthu amanena zochokera pansi pamtima. Ndichitenji?
MC,
Blantyre

MC,
Zikuoneka kuti izi nzongoseleula chifukwa palibe pamene mwanenapo kuti adakambapo kuti akusiyani chifukwa ndinu wosaoneka bwino. Iyo ikadakhala nkhani ina. Momwe mwafotokozera, izi zimakusautsani choncho ndi bwino kumuuza maso ndi maso kuti izi zimakudetsani kukhosi. Kukambirana ndiko kumatha zonse.

Ndi mwana
Gogo,
Ndili ndi zaka 24 ndipo zibwenzi zanga zakhala zikumangotha. Koma masiku amenewa mnyamata wina akuonetsa chidwi pa ine. Vuto ndi lakuti iyeyo kwa ine ndi mwana ndiye ndikamuuza, iye amakakamirabe. Ndi chitenji?

Mtsikana wanu
Msungwana,
Chikondi chenicheni si chiona msinkhu. Nkuthekatu kuti ‘mwanayo’ ali ndi chikondi chimene simungachipeze kulikonse. Ngakhale mutazemba chotani koma ngati Mulungu adakulemberani kuti wanu ndi ‘mwanayo’ inu mungaletse? Chofunika apa nkuonetsetsa kuti zolinga ndi zofuna zake nzotani. Pali achinyamata ena a ulesi amene masiku ano akufuna amayi okulirapo cholinga adye nawo chuma. Ichi si chikondi. Mumuonetsetse kuti akufuna chiyani kwa inu, musanapange chiganizo.akukhululuka

Gogo,
Ndili ku Nsanje ndipo ndili ndi chibwenzi ku Blantyre. Anzanga ena amamuimbira foni kumandiipitsira mbiri kuti ndili ndi zibwenzi zambiri. ndikamutumizira uthenga komanso kumuimbira foni sakumayankha ngati kale. Chibwenzi wathetsa ngakhale ndakhala ndikupepesa. Sakukhululuka ngakhale ndikufuna tibwererane.
SL,
Nsanje.

SL,
Fupa lokakamiza limaswa mphika, akulu akale adatero. Apa zikuonetseratu kuti chidwi mwa inu mwamunayo palibe, chatheratu. Ngati nzoona kuti inu palibe chimene mudalakwa koma a vundula madzi, mtima wanu usavutike chifukwa mudzapeza mwamuna wina. Apa musatayepo nthawi munamukonda mwamuna koma poopa kuswa mphika mutayeni. Iyetu akuoneka kuti ngotengeka ndi za m’maluwa. Adzakupatsani mavuto.

Ofuna mabanja
Ndine mkazi wa zaka 34 ndikufuna mwamuna wa zaka 35 kumapita kutsogolo. 0998 501 0901

Ndili ndi zaka 26 ndipo ndimayendetsa minibasi. Ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 18 ndi 22. 0999 031 842

Ndili ndi zaka 23 ndikufuna mkazi wa zaka za pakati pa 18 ndi 20. Akhale wochokera kumwera.
0995 492 657

Ndine mkhristu wa zaka 26 ndipo sindinakwatirepo. Ndikufuna mkazi woopa Mulungu yemwe ndiwokonzeka kukayezetsa magazi tisanakwatirane. 0994 396 005

Ndili ndi zaka 34 ndipo ndikufuna mayi wa zaka 45 kumapita kumtunda. 01 11 642 230

Ndili ndi zaka 30 ndipo ndikufuna mwamuna wa SDA. Ndili ndi ana awiri. 0884 438 309

Ndikufuna mkazi womanga naye banja. Ndili ndi zaka 25. 0884 538 532

Ndili ndi zaka 31 ndikufuna mkazi wa chibwenzi. 0885 331 478.

Related Articles

Back to top button
Translate »