Chichewa

Bishopu aganiziridwa kugwiririra mwana

Listen to this article

Madzi achita katondo pa mpingo wa Assemblies of Fountain ku Chileka m’boma la Lilongwe komwe bishopu wa mpingowu Alexander Selemani ali m’manja mwa apolisi pomuganizira kuti adagwiririra mwana wa mbusa wa mpingowu.

Selemani, yemwe adayambitsa mpingowu, ndi mphunzitsi pa sekondale ya Chileka m’bomalo.

Mneneri wa polisi m’boma la Lilongwe, Foster Benjamin, adati Selemani akumuganizira kuti adachita za chipongwezi mu March chaka chino.

Benjamin adati Selemani adapempha mwanayu kuti akamuthandize ntchito zapakhomo popeza mkazi wake adapita kumudzi kukachira.

An artist’s impression of court proceedings

Koma atafika ku nyumbako, mkuluyu akuganiziridwa adamugwiririra mtsikanayo mpaka kumupatsa mimba.

Selemani amayembekezeka kukaonekera ku bwalo la milandu Lachinayi pa July 9 2020.

Izi zachitika pamene bambo wina wa zaka 47 akumuganizira kuti wagwiririranso ana 7 a zaka zapakati pa 8 ndi 11 m’boma la Dedza.

Levison Manyozo akumuganizira kuti adagwiririra anawo kuyambira chaka chatha.

Iye akumuganizira kuti amagwirira anawa powanyengerera ndi masuwiti ndi mabisiketi akapita ku golosale kwake kukagula katundu.

Mneneri wa polisi m’boma la Dedza, Edward Kabango, watsimikiza za nkhaniyi.

Kabango adati nkhaniyi yatulukira poyera pamene anawo amasewera ndipo m’modzi wa iwo adauza anzake kuti bamboyo amamugwiririra.

“Anzakewo adauluranso kuti nawonso amawagwiririra akapita ku golosale kwa mkuluyu.

“Mwamwayi pamalopo pamadutsa mkulu wina yemwe adamva nkhaniyo ndi kukatsina khutu makolo a anawo,” adatero Kabango.

Mneneriyu adati umboni wochokera ku chipatala cha Dedza waonetsa kuti mkuluyu amachita anawo za chipongwezo.

Manyozo amachokera m’mudzi mwa Mkumayani, Mfumu Kasumbu, m’boma la Dedza.

Kugwiririra ana sikudasiye mbali chifukwa mtsikana wina wa zaka 15 wagwiriridwanso ndi anyamata awiri m’boma la Nkhotakota.

Wachiwiri kwa mneneri wa polisi m’boma la Nkhotakota, Paul Malimwe, watsimikiza za nkhaniyi.

Iye adati Uzeni Banda wa zaka 18 ndi David Francis wa zaka 26 adagwiririra mwanayu pamene ankapita ku golosale kukagula zinthu.

Anyamatawa atakumana ndi mtsikanayu adamukokera patchire n’kumuchita chipongwe.

Anyamatawa amachokera m’mudzi mwa Muyanja, Mfumu Nkhanga, m’boma la Nkhotakota.

Related Articles

Back to top button
Translate »