Chichewa

Blessings Cheleuka wa pa JOY FM

Listen to this article

Amalawi ambiri kuyamba Lolemba mpaka Lachisanu nthawi ya 2 koloko kufika 4 koloko masana amatsegula wailesi ya Joy FM kuti amvere nyimbo zothyakuka zoimbidwa ndi Amalawi anzawo. Namandwa wophulitsa nyimbo zimenezi ndi Blessings Cheleuka, yemweso wachitapo mbali yaikulu kutukula alakatuli m’dziko muno. STEVEN PEMBAMOYO adacheza naye motere:

Cheleuka: Chilichonse nchotheka  pamoyo wa munthu
Cheleuka: Chilichonse nchotheka
pamoyo wa munthu

Dzifotokoze mkulu wanga.

Ine ndine Blessings Cheleuka, ndimachokera m’mudzi mwa Mothiwa kwa T/A Likoswe m’boma la Chiradzulu. Ndine muulutsi wa pawayilesi komanso ndimakonda ndakatulo kwambiri.

Ntchito yakoyi udayamba liti?

Ndakhala ndikugwira ntchitoyi kwa zaka 12 ndipo ndagwira m’nthambi zosiyanasiyana monga wolemba nkhani, mkonzi, muulutsi ndi zina. China choti mungadziwe n’chakuti ndagwirako ntchitoyi kunyuzipepala ndi kuwayilesi komwe ndiye ndili ndi ukadaulo kwambiri.

Akadaulo ambiri amakhala ndi komwe adaphunzirira ntchito, iwe udaphunzirira kuti?

Choyamba, ndidaphunzira zautolankhani kusukulu yaukachenjede ya Polytechnic, nthambi imodzi ya University of Malawi. Kumeneku ndidaphunzira zomwe zimatenga kuti munthu ukhale mtolankhani mbali zonse. Kuchoka apo m’malo momwe ndakhala ndi kugwira ntchito monga Power 101 FM komwe ndidayambira ntchito; ndidaphunzirako za kuulutsa mapologalamu osanjenjemera chifukwatu kunena zoona ndi luso lapadera limenelija. Ndimayamikaso Mulungu ponditsogolera ndi kundiunikira.

Nanga umaulutsa mapologalamu anji pawailesi?

Ndimaulutsa mapologalamu ambiri monga Dimba Music yomwe imauluka kuyambira Lolemba mpaka Lachisanu nthawi ya 2 koloko masana mpaka 4 koloko madzulo; Zina Ukamva yomwe imauluka 8 koloko madzulo Loweluka; pologalamu ya ndakatulo yotchedwa Patsinde yomwe imayamba 8 koloko mmawa mpaka 10 koloko; Mfuwu Wa Chimwemwe kuyamba 6 koloko mpaka 9 koloko mmawa Lamulungu; ndi Gospel Top 20 ya nyimbo za uzimu komanso ndine ndimayang’anira za uwulutsi kuwailesi ndi kanema za Joy.

Ukutinso uli ndi chidwi pa zaulakatuli, umatengapo gawo lanji?

Ndapanga zambiri monga kudzera mu pologalamu yanga ya Patsinde. Ndimafukula alakatuli omwe sadayambe kudziwika. Ndimakonzaso zochitika za alakatuli ndipo anthu ambiri amazikonda.

Ukafatsa umakonda kutani?

Ndimakonda kuonerera mapologalamu a pakanema ndi zauzimu basi.

Mwina okutsata amangoti ndiwe muulutsi, ungawauzenji za iwe?

Ine ndine Blessings Cheleuka odziwika kuti ‘Bule wanu’ pazausangalatsi ndipo cholinga changa nkusangalatsa Amalawi basi.

Chikhulupiriro chako n’chotani?

Ndimakhulupirira kuti chilichonse nchotheka pamoyo wa munthu, chofunika n’kulimbikira basi. n

Related Articles

Back to top button
Translate »