Chichewa

Boma lapempha amalawi adekhe pa za mathanyula

Listen to this article

 

Boma lapempha aMalawi kuti adekhe pankhani yoimitsa lamulo loletsa umathanyula m’dziko muno.

Polankhulapo mkati mwa sabatayi, mneneri wa boma Jappie Mhango adati kuthamanga si kufika ndipo nkhaniyo ifunika iunikidwe bwino ndi akatswiri a za malamulo.

Mhango adati masiku akubwerawa Amalawi apereka maganizo awo pankhani ya mathanyulayi ponena kuti atolankhani ndiwo akukokomeza polemba ndi kuulutsa zambiri zokhudza nkhanizi.

Mneneriyu adauza Tamvani kuti boma lapanga chiganizo chopereka nkhaniyo kwa akatswiriwo kuti akamaliza kuunika alengeze zomwe Amalawi akuyenera kuchita pankhaniyi.

Adachititsapo chinkhoswe: Chimbalanga (kumanja) ndi Monjeza
Adachititsapo chinkhoswe: Chimbalanga (kumanja) ndi Monjeza

“Tikufuna kutsatira ndondomeko zoyenera, tisathamange ayi,” Mhango adatero, nkuonjezera kuti akatswiri a zamalamulowo ndiwo alangize boma pa ndondomeko yoyenerayo.

“Mundimvetsetse, sindikuti tikhala ndi riferendamu, ayi, koma ndikuti atilangiza pa za ndondomeko zoyenera kutsatidwa kuti Amalawi apereke maganizo awo pankhaniyo,” adatero Mhango.

Koma padakalipano zipani zotsutsa boma komanso mafumu adzudzula boma poimitsa lamulo lomanga amathanyula lisanamve maganizo a anthu a m’dziko muno.

Polankhulapo m’sabatayi, wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha People’s Party Kamlepo Kalua adati izi zikukhala ngati kutengera Amalawi konyongedwa.

Kalua adati umathanyula ndi khalidwe losemphana ndi zomwe chikhulupiriro ndi chikhalidwe chawo chimanena.

“Kodi mukundiuza kuti tivomereze umathanyula ndi kusiya chikhulupiriro chathu chifukwa cha thandizo lochokera kunja? Apatu tikupita kokanyongedwa ndithu,” adatero Kalua.

Iye adati Amalawi aone zakutsogolo osati zalero chifukwa umathanyula udzapha tsogolo la dziko lino.

“Ndalamazo mudya lero, ndipo musangalala, koma ganizani za tsogolo lanu,” Kalua adatero.

Koma Inkosi ya Makhosi M’mbelwa adati ngakhale mafumu sadakhale pansi kukambirana za nkhaniyi chifukwa chosowa thandizo, sakuvomereza zoimitsa lamulo loletsa umathanyula m’dziko muno.

M’mbelwa adati umathanyula ukusemphana ndi chikhalidwe cha Amalawi ndipo si zololedwa.

“Masiku akubwerawa tikumana ngati mafumu kuti nafe tilankhulepo pankhaniyi, yomwe yautsa mapiri pachigwa,” M’mbelwa adatero.

Sabata yatha mneneri wa chipani cha PP Ken Msonda, polankhula mwa yekha adati Amalawi ayenera kupha ochita mathanyula. Bungwe la maloya m’dziko muno la Malawi Law Society (MLS) lidati apa Msonda adalakwa ndipo lidati Msonda ayenera kumangidwa.

Bwalo la milandu la majisitileti ku Blantyre laitanitsa Msonda kuti akaonekere kubwalolo pa 22 January.

Koma polalikira kumpingo wa South Lunzu CCAP ku Machinjiri mumzinda wa Blantyre, Msonda adati sasintha mawu ake. “Iyi si nkhondo ya Msonda koma nkhondo ya ana a Mulungu kulimbana ndi mdyerekezi,” adatero iye mu ulaliki wake.

Izi zili choncho, mmodzi mwa omenyera ufulu wa anthu Gift Trapence adati ochita mathanyula ali ndi ufulu wachibadwidwe ndipo Amalawi sayenera kupondereza anthuwa.

“Malamulo oyendetsera dziko lino komanso malamulo a dziko lapansi amaneneratu kuti si bwino kuphwanya ufulu wa ena,” adatero Trapence.

Nkhani ya mathanyula yayala nthenje kuchokera pamene anyamata awiri Kelvin Gomani ndi Cuthbert Kulemeka adagwidwa ndi apolisi powaganizira kuti amachita za u ndevu ku ndevu.

Maiko ndi mabungwe othandiza dziko lino adati aleka kupereka thandizo kudziko lino ngati awiriwo satulutsidwa. Boma lidatulutsa awiriwo.

Aka si koyamba kuti boma litulutse amathanyula litakakamizidwa ndi a kunja. Mmbuyomu, boma lidatulutsa Tiwonge Chimbalanga ndi Steven Monjeza mkulu wa bungwe la United Nations Ban ki Moon atabwera m’dziko muno kudzalikakamiza kutulutsa awiriwo. n

Related Articles

Back to top button
Translate »