Nkhani

Boma libweza moto pa zolipiritsa m’zipatala

Listen to this article

Ganizo la boma loyambitsa mbali yolipiritsa m’zipatala zonse za boma kuyambira July akubwerayu, lalephereka, nduna ya zaumoyo, Peter Kumpalume, yatero.

Izi zikutanthauza kuti zipatala za boma m’maboma zikhalabe zaulere, monga zakhala zikuchitikira.hospitalZitamveka kuti boma likufuna kuyambitsa mbali yolipiritsa m’zipatala zonse za boma, anthu ena, mafumu komanso amabungwe sadasangalale ndi mfundoyo ndipo adapempha boma kuti lisayerekeze kubweretsa chilinganizochi.

Koma ngati kubwezera madzi kumkobwe, Kumpalume pano wati muunduna wake mudalibe ganizo lofuna kukhala ndi mbali ina yolipitsa m’zipatala, mawu omwe akutsutsana ndi zomwe mneneri wa undunawu, Adrian Chikumbe, adauza Tamvani sabata zitatu zapitazo.

“Nkhaniyi ikungokambidwa koma mosatsatira bwino mutu wake. Monga ndikudziwira, muunduna wanga mulibe ganizo lotere,” adatero Kumpalume pouza nyuzi ta Weekend Nation ya Loweruka lapitali.

Kalata yosayinidwa ndi mabungwe monga Oxfam, ActionAid, Save the Children, Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), National Association for People Living with HIV and Aids in Malawi (Napham), Medicines Sans Frontiers (MSF) and Development Communication Trust (DCT) idandauza boma kuti ganizo lokhala ndi mbali yolipitsa ivulaza anthu osauka.

Timothy Mtambo wa CHRR, adati anthu ovutika apitirira kuvutikabe chifukwa kumbali yaulere kukhala kopanda zipangizo zokwanira poyerekeza ndi kolipira.

“Chidwi chizikhala kwa anthu olemera osati osauka, apa ndiye kuti osauka apitirira kusaukira,” adatero Mtambo, ganizoli litangoululika.

Lero Mtambo ndi wokondwa kuti boma lasintha ganizoli.

“Iyi ndi nkhani yabwino, pakutha pa zonse, ovutika adakakhala anthu ovutikitsitsa. Apa ndiye kuti zili bwino,” adatero pothirapo ndemanga pa ganizo la boma losintha maganizo ake.

Related Articles

Back to top button
Translate »