Nkhani

Boma lifalitsa lipoti la zotaya mimba

Listen to this article

Boma latulutsa lipoti la zotsatira za kafukufuku wa wokhudza za Malamulo ochotsa mimba yemwe bungwe lapadera lofufuza za malamulowo lidachita mu 2015.

Lipotilo lidaperekanso maganizo ake kuti Malamulo okhudza kuchotsa mimba asinthidwe kuti azilola amayi amene atenga pakati atagwiriridwa, ngati mayi atenga mimba atagonana ndi mbale wake, komanso ngati mimba ingadzetse paumoyo ndi maganizo a mzimayi. Padakalipano Malamulo a dziko lino amangolola kuchotsa mimba ngati iyika pachiopsezo moyo wa mayiyo.

Chavula kuonetsa lipotilo

Wachiwiri kwa mkulu wa zosintha Malamulo ku Law Commission, Edda Chavula, unduna wa zamalamulo udzatulutsa bilo yokhudza msinthowo ndipo aphungu a kawakambirana.

“Takondwera kwambiri chifukwa boma tsopano lavomereza lipotilo, limene a Law Commission adachita atatumidwa ndi Unduna wa Zaumoyo,” adatero Chavula.

Mwa zina, lipotilo lidapeza kuti kuli imfa zochuluka za amayi ofuna kuchotsa pakati mobisa amene amagwiritsa zinthu zina monga zitsamba, mitengo, mawaya ndi zina zotere. Amayiwo akapita kuchipatala, achipatala amakachotsa zotsalira za khanda lotaidwalo koma ena amapita kuchipatala mochedwa, zimene zimadzetsa imfa.

Mkulu wa mabungwe ounikira kuti amayi asamachotse pakati moika miyoyo yawo pachiswe la Coalition for the Prevention of Unsafe Abortions (Copua) Simon Sikwese adati akondwa ndi kuvomereza kwa lipotilo.

“Takondwa ndipo tikuyembekeza kuti aphungu adzakambirana za lamuloli mtsogolomu. Malamulo amene alipo pano amaika pachiopsezo miyoyo ya amayi ndi asungwana,’ adatero Sikwese.

Malinga ndi kadaulo wa zaumoyo wa amayi Dr Chisale Mhango wa ku College of Medicine, kafukufuku adasonyeza kuti mimba 141 000 zidachotsedwa mu 2015.

“Ngati madotolo komanso a zakafukufuku, tidapeza kuti chipembedzo sichilepheretsa amayi kuchotsa mimba. Ngakhale Malamulo akhwime chotani, amayi amachotsabe mimba. Izi zimangochititsa kuti achotse mimbazo modzivulaza,” adatero Mhango. 

Related Articles

Back to top button
Translate »