Chichewa

Boma liganizire bwino pa sabuside

Listen to this article

Adzavutika: Nkhalamba ndi ana amasiye

Mkonzi,

Ndalemba kalatayi kutsatira zomwe nduna yoona zaulimi a Allan Chiyembekeza adanena masiku apitawa.

Mukunena kwawo, a Chiyembekeza adati boma likufuna kuti anthu omwe angalandire mbewu ndi fetereza zotsika mtengo chaka chino asalandirenso chaka chinacho.

Iwo akuti izi zithandiza kuthetsa mchitidwe wa chinyengo komanso kuchepetsa mchitidwe woti anthu amodzimodzi ndi amene azipindula mundondomekoyi.

Adzavutika: Nkhalamba ndi ana amasiye
Adzavutika: Nkhalamba ndi ana amasiye

Ngakhale maganizo amenewa akuoneka ngati abwino, ine ndikuona kuti mfundoyi ipweteketsa magulu ena a anthu.

Ndikunena izi chifukwa boma silidatiuze ndondomeko zomwe liike pofuna kuonetsetsa kuti okalamba ndi ana amasiye omwe amalerana okhaokha omwe sangathe kudzigulira feteleza ndi mbewu pamsika liziwathandiza bwanji.

Palinso anzathu omwe ali ndi mavuto osiyanasiyana monga kulumala omwe akhala akudalira feteleza ndi mbewu zotsika mtengo kuti apeze kachakudya kokwanira timisiku tingapo kudzera mu ulimi.

Awa ndi ena chabe mwa magulu a anthu omwe sangathe kudzigulira mchere wam’nthaka ndi mbewu pamsika pomwe thumba limodzi la feteleza panopo ndi cha pakati pa K22 000 ndi K23 000.

Choncho, ndikufuna ndifunse boma kudzera kwa a Chiyembekeza kuti litiuze ndondomeko yomwe lakonza poonetsetsa kuti anthu akuthandizika pamene boma likugwiritsa mfundo yoti munthu yemwe wapindula chaka chino asadzapindulenso chaka chinacho.

Samson Kandondo Phiri,

Lilongwe

Related Articles

Back to top button