Chichewa

Boma likonzekera Ebola

Listen to this article

Unduna wa zaumoyo wasonjola komiti yoyang’anira za kapewedwe ndi kuthana ndi matenda a ebola kuti ikhale chile zitamveka kuti matendawa abuka

m’dziko la Democratic Republic of Congo (DRC).

Scanning for Ebola

Malingana ndi undunawu, kuyambira mwezi wa April, 2017, anthu 11 apezeka ndi matendawa m’dzikolo ndipo mwa  anthuwa, atatu adamwalira nawo zomwe zikupereka nkhawa kuti akhoza kusefukira m’maiko oyandikana nawo.

Dziko la DRC ndi dziko lomwe maiko osiyanasiyana kuphatikizapo Malawi amatumizako asilikali ankhondo kukathandiza kukhazikitsa bata malingana nkuti mdzikoli muli nkhondo yamgonagona.

Mkulu oyang’anira ntchito zaumoyo mu unduna wa zaumoyo m’dziko muno Charles Mwansambo wati komitiyi yayamba kale kugwira ntchito yake ndipo wapempha anthu kuti agwirane manja ndi komitiyi kuti matendawa asafike m’dziko muno.

“Komiti imeneyo yayamba kale kukumana ndi kukonza ndondomeko zoyenera. Padakalipano tayamba kale kuunika anthu olowa m’dziko muno kuti ngati ali ndi matendawa abwezedwe ndipo mauthenga akumwazidwa moyenera,” watero Mwansambo.

Chikalata chomwe undunawu watulutsa, chikukumbutsa anthu kuti nthendayi ndiyopatsirana ndipo imafala kudzera mu kukhudzana ndi madzi a m’thupi mwa munthu amane ali ndi matendawa kapena zinyama zina zomwenso zimapezeka ndi matendawa.

Icho chati matendawa akagwira munthu, amamva zizindikiro monga kutentha thupi, kufooka, kuwawa kwa minofu, kuwawa kwa mutu ndi zilonda za pakhosi zomwe zimatsatana ndi kutsegula, kusanza, zidzolo ndi kulephera kugwira ntchito bwino kwa chiwindi ndi kapamba ndipo nthawi zina magazi amatsanyukira mkati kapena kunja kwa thupi.

Undunawu wati anthu akuyenera kusamala podwazika matenda omwe akuonetsa zizindikiro za matendawa komanso akuyenera kusamala poika maliro a munthu yemwe wamwalira ndi matenda a Ebola kuti asatengere.

Matenda a Ebola ndi amodzi mwa matenda omwe mankhwala ake sadapezeke mpaka pano ndipo unduna wa zaumoyo wati mankhwala ake aakulu n’kupewa kutenga potsata malangizo a za kapewedwe.

Matendawa adabukanso m’chaka cha 2014 ndipo adasautsa m’maiko ambiri ndi kupha anthu ochuluka koma chifukwa cha kugwirizana kwa maiko kudzera mu thambi ya zaumoyo ya World Health Organisation (WHO), matendawa adagonja. 

Related Articles

Back to top button
Translate »