Chichewa

Boma likonzekera el nino—chilima

Listen to this article

 

Boma lati alimi ndi anthu m’dziko muno asanjenjemere ndi lipoti la nthambi ya zanyengo loti chaka chino kukhoza kukhala mphepo ya El Nino ponena kuti zikachitika ilo ndi lokonzeka kuthana ndi mavuto amene angadze.

Wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino, Saulos Chilima, adalengeza posachedwapa pamsonkhano wa atolankhani pofuna kupereka chilimbikitso kwa alimi ndi anthu onse.

Chilima:Boma litumiza alangizi ndi achitetezo m’madera osiyanasiyana
Chilima:Boma litumiza alangizi ndi achitetezo m’madera osiyanasiyana

“Takhazikitsa thumba la ndalama zokwana K1 biliyoni zoti zitithandize kukonzekera mphepo imeneyi kuti isadzaononge,” adatero Chilima.

Chilima adati ndalama zomwe boma lakhazikitsazi ntchito yake n’kudzalimbana ndi mavuto monga kusefukira kwa madzi kapena ng’amba zitati zachitika potsatira mphepo ya El Nino yomwe ikumvekayi.

Iye adati pokonzekera El Ninoyu, boma litumiza alangizi ndi achitetezo m’madera osiyanasiyana kuti mphepoyi itati yafika adzakhale athandizi a anthu populumutsa katundu ndi miyoyo ya anthu.

El Nino ndi mphepo yomwe imasokoneza ntchito za ulimi chifukwa chosapanganika. Nthawi zina mphepoyi imachititsa kuti mvula igwe yoononga pomwe nthawi zina imachititsa ng’amba.

Mneneri wa unduna wa zamalimidwe Erica Maganga adati mvula ikagwa mopitirira muyeso, mbewu zimakokoloka pomwe kukachita ng’amba mbewu zambiri zimalephera kucha.

Iye adati njira ziwirizi zimabweretsa vuto la njala ndi umphawi m’dziko chifukwa anthu amakhala opanda chakudya ndi choti angagulitse kuti athandizike.

Chaka chatha mbewu zambiri zidakokoloka ndi madzi mvula itabwera moonjeza panthawi yochepa koma akatswiri adati izi sizidali zotsatira za mphepo ya El Nino koma kusintha kwa nyengo.

Mneneri wa nthambi yoona za nyengo, Sute Mwakasungula, wati anthu azitsatira zomwe nthambiyi ikunena pa mmene nyengo ikuyendera ndi kutsatira malangizo omwe nthambiyi ikupereka.

Iye adati mphekesera zina zomwe zimamveka pankhani yokhudza za nyengo zikhoza kusokoneza anthu, makamaka alimi omwe amakhala ndi nkhawa kuti mpamvu ndi zipangizo zawo zikhoza kupita pachabe.

“Nthambi yathu ili ndi akatswiri omwe amadziwa momwe nyengo ikhalire ndipo amapereka malangizo a zomwe anthu angachite kuti asakhudzidwe kwambiri. Anthu azitsatira zimenezi,” adatero Mwakasungula.

Alimi ena ati boma likuyenera kumafotokoza pafupipafupi zokhudza mphepoyi kuti iwo asadzadzidzimutsidwe.n

Related Articles

Back to top button
Translate »